61
1 TANTHAUZO LA SURAT AL FATIHAH Wolemba: Muhammad Abdul Karim Duncan

Ndime7 (Surat Al Fatehah)

  • Upload
    malawiu

  • View
    255

  • Download
    7

Embed Size (px)

DESCRIPTION

The Exegesis of the first chapter of the Holy Qur'an in local Malawian Language (Chichewa).By Brother Muhammad Abdul Karim Duncan - Malawi Ummah-----Special thanks to:Sheikh Hassan DullahSister Jamila Ja'farBrother Ramadhan Issah

Citation preview

Page 1: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

1

TANTHAUZO LA SURAT AL FATIHAH

Wolemba:

Muhammad Abdul Karim Duncan

Administrator
Typewriter
Malawi Ummah
Page 2: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

2

__________________________

TANTHAUZO LA SURAT AL FATIHAH

Wolemba:

Muhammad Abdul Karim Duncan

Page 3: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

3

Chitetezo cha bukuli

Gawo lirilonse la bukuli silikuloredwa kusindikizidwa

kachiwiri popanda chilorezo cholembedwa

kuchokera kwa mlembi kapena

msindikizi.

[email protected]

[email protected]

MALAWI UMMAH

www.malawiummah.com

Page 4: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

4

ZA NKATIMU

Mawu oyamba………………………………......….............…5

Surat Al Fatihah…………………………………………......10

Ndime 1………………………………………………........….13

Bismillah………………………………………....….........15

Al Rahman Al Rahim………………………...….……......17

Ndime 2…………………………………………….…............22

Al Hamdulillah……………………………….……......….22

Rabbil ‘alamin……………………………….…...…....…26

Ndime 3……………………………………....………..……...30

Al Rahman Al Rahim…………………….………….….…......30

Ndime 4…………………………….……………..…..............31

Yawmiddin…………………………..................………....34

Din…………………………………….……...……...…...40

Ndime 5…………………………………….…………..…..…44

Iyyaka na’budu…………………………............................45

Wa iyyaka nasta’in……………………………...…......….46

Ndime 6……………………………………………..…..…….49

Ihdinas siraatal mustaqim……………………………….……49

Ndime 7…………………………………………..……..…….53

Siraatalladhina an’amta ‘alayhim……………..……........53

Ghayril magh-dhubi ‘alayhim…………………..…..….....57

Waladh-dhaallin………………………………..…..……..58

Ameen…………………………………….…….…….....……59

Page 5: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

5

�سم ن اهللا

ح� الر

الر

M'dzina la Mulungu Wachifundo Chambiri, Wachisoni.

MAWU OYAMBA

Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, amene adabvumbulutsa

Buku lolemekezeka la Quran, lomwe likufotokoza za chinthu

china chirichonse mwatsatanetsatane. Mtendere ndi madalitso

zipite kwa Mtumiki womaliza Muhammad (SAW) pamodzi ndi

omutsatira ake onse kufikira pa tsiku lachiweruzo.

Mulungu adabvumbulutsa Quran kuti imutsogolere munthu

muchowonadi, imupezetse madalitso ndi mtendere,

iwachenjeze anthu ochimwa za moto wa Jahannam, komanso

nkhani yosangalatsa ya Jannah kwa ochita zabwino.

ليك

ناعل نز

و

اب�ت

انا ال

ء ل�ل تبي هدى �

ة و

ر

ى و

��

و

مسلمني )89( لل

“…Ndiponso takuvumbulutsira Buku ili lomwe likufotokoza za

chinthu chirichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere

ndiponso ndi nkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Mulungu).”

Kuyang’ana chabe mawu a mu Quran kumabweretsa madalitso,

sitikufunikira kulekera pomwepo, koma tiyeneranso

kuyiwerenga chifukwa kuwerenga Quran kumabweretsa

madalitso komanso malipiro abwino pa chilembo chirichonse

Page 6: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

6

chimene munthu akuwerenga. Tisangowerenga chabe koma

tikufunikanso kuphunzira matanthauzo, tikadziwa matanthauzo

tisayimire pomwepo koma kugwiritsa ntchito zimene tamva.

Pomaliza tiyenera kuchedwa ndi kulingalira mau a Mulunguwa

ndime ndi ndime, liwu ndi liwu, mukuchita zimenezi

tidzazindikira kuti Quraniyi yafotokozadi za chinthu china

chirichonse. Tidzapeza kuti moyo wathu wonse wa tsiku ndi

tsiku uli mu Quran, zinthu zonse zamakono (Science) za

mitundu yonse tizipeza zili mu Quran. Koma zonsezi kuti

tizipeze mu Quran tiyenera kulingalira ndi kuganiza mozama za

matanthauzo a Quran, zimenezo ndizomwenso Mulungu

akutilamulira mu Surah 38 (Saad) ndime 29:

اب كت

ناه

ل

ز

إليك أن

ك

ار

ب

وا م

بر د

اته لي آي

ر ذك

ت

لي

اب أولو و

ب

ل

)29( األ

“(Ili), ndibuku lochuluka madalitso lomwe talivumbulutsa kwa

iwe kuti (anthu) azame kwambiri pomvetsetsa ndime zake; ndi

kuti apeze nalo phunziro eni nzeru.”

Tikulamulidwa kuti tizame pomvetsetsa matanthauza a Quran,

mukutero tiphunzira zinthu zambiri.

Mwachitsanzo, tikamafuna kuyeza kutalika kwa chinthu

chaching’ono timagwiritsa ntchito ma Millimetre (mm),

chokulirapo timagwiritsa ntchito ma Centimetre (cm).

Chachitali kwambiri timagwiritsa ntchito ma Metre (m). Mtunda

ukatalika kwambiri timagwiritsa ntchito ma Kilometre kapena

ma Mile.

Page 7: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

7

Zonse tatchulazi zikugwiritsidwa ntchito poyeza mtunda

wochoka malo kufika malo ena. Tikamawerenga ma buku omwe

amakamba za m’lengalenga, amatiuza kuti mtunda wochoka

Galaxy (gulu la nyenyezi) kukafika Galaxy ina ndiwautali

kwambiri, choncho m’malo mogwiritsa ntchito zoyezera mtunda

timagwiritsa ntchito chimodzi mwa zoyezera nthawi chomwe

chiri chaka, chimatchedwa kuti “Light Year1.” Izi zili choncho

chifukwa mtunda wautali kwambiri umayezedwa pogwiritsa

ntchito nthawi.

Tikawerenga Surah 3 (Aali ‘Imran) ndime 30, tikupeza kuti

Quran ndi imene idayambilira kugwiritsa ntchito nthawi poyeza

mtunda anthu a Science asadazitulukire:

وم

د ي

وء تو

من س

ملت

ا ع

م

ضرا و

ح م

من خري

ملت

ا ع

س م

لو أن تجد كل نف

ينه ب

ا و

ي�

دا ب

عيدا أم

ب

كم

ر ذ

ح

ي

و

ه اهللا

س

نف اهللا

و

وف

ء

اد ر

عب

)30(بال

"Tsiku lomwe mzimu uliwonse udzapeza zabwino zomwe

udachita zitabweretsedwa, ndiponso zoipa zomwe udachita;

udzalakalaka kuti pakadakhala mtunda wautali pakati pa

machimo ake ndi iye. Ndipo Mulungu Mwini akukuchenjezani za

chilango Chake. Ndipo Mulungu ndiwoleza kwa akapolo Ake.”

1Light Year ndi mtunda womwe kuwala (Light) kumayenda pa chaka chimodzi.

Timamva kuti kuwala kumatha mtunda wokwana pafupifupi 300,000km mu second imodzi, ndiye kuti pa chaka chimodzi kuwala kumatha mtunda wokwana pafupifupi 9,460,800,000,000km. Kuchoka pa Galaxy yathu kufika pa Galaxy yomwe yayandikana nayo kwambiri pali mtunda wokwana 180,000 Light Year. Kuti tiyike mma Kilometres itipatsa nambala yaitali kwambiri, choncho tagwiritsa ntchito nthawi poyeza mtunda.

Page 8: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

8

Titenge mawu oti: “Udzalakalaka (mzimu) kuti pakadakhala

mtunda wautali pakati pa machimo ake ndi iye.”

Mawu oti: “عيدادا ب

amadan ba’idan” ndi amene akutathauza أم

kuti mtunda wautali. Tanthauzo lenileni la mawu amenewa

m’chichewa ndi “Nthawi yaitali” koma otanthauzira akutiwuza

kuti “Mtunda wautali.” Quran yagwiritsa ntchito nthawi poyeza

mtunda.

Quran yagwiritsa ntchito nthawi ponena zamtunda umene

munthu akalakelake kuti atalikane ndi machimo ake, chifukwa

chakuti mtunda wake ndiwautali kwambiri siwungayezedwe ndi

ma metre kapena ma kilometre.

Choncho amene awerenge chabe tanthauzo la ndimeyi adziwa

kuti ndi mtunda wautali, koma amene awerenge ndikulingalira

tanthauzolo mozama adziwa kuti mtundawu ndiwautali koposa,

ndipo akhala woopa kuti ngati munthu akalakelake kuti

atalikane ndi machimo ake mtunda ngati umenewo ndiye kuti

machimowo adzakhala oipa kwambiri choncho adzakhala

wopewa machimo ndi woopa Mulungu. Ndichifukwa chake

timapeza ndime 28 mu Surah 35 (Faatir) ikutiuza kuti:

شى

خاي

إنم

اده من اهللا عب

اء

علم

)28(...ال

“…Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Mulungu mwa akapolo

Ake.”

Page 9: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

9

Chifukwa chakuti odziwawo akudziwa zomwe zili m’kati mwa

ndime zimenezi choncho amakhala oopa.

Choncho ndikofunikira kuti tidzilingalira ndi kuzama

pomvetsetsa mawu a mu Quran.

Chifukwa chakuti Surat Al Fatihah ndi Surah yoyamba komanso

ndi imene pafupifupi aliyense amawerenga pa Salat, ndidaona

kuti ndichanzeru kuyamba kulemba ndikufotokoza matanthauzo

ake. Bukuli lomwe ndidayamba kulemba pa 1 Muharram 1435

Hijri, pomwe padali pa 5 November 2013, likutchedwa kuti:

“Ndime7” kutengera nambala ya ndime za Surayi.

Ndikuthokoza mwapadera anthu awa amene ndimathandizana

nawo kuti buku limeneri litheke: Sheikh Hassam Dullah,

Jamila Jafar ndi Ramadhan Issah. Tikupempha Mulungu kuti

ationjezere kuzindikira ndi nzeru ndikuti uthenga umenewu

ukhale wothandiza ndi wa phindu pa dziko pano komanso moyo

uli nkudza, Ameen.

____________________________

Muhammad Abdul Karim Duncan

Al Azhar University

Page 10: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

10

�سم ن اهللا

ح� الر

الر

SURAT AL FATIHAH

Surat Al Fatihah ndi Surah yachisanu (5) kutsika

(kubvumbulutsidwa) kwa Mtumiki Muhammad (SAW)1, koma

ndi Surah yoyamba mundondomeko ya Buku la Quran. Surayi

ili ndi ndime (Ayah) zokwana zisanu ndi ziwiri (7). Mu Salah

zonse zisanu patsiku, munthu amawerenga Surayi kokwana

khumi ndi kasanu ndi kawiri (17) patsiku. Surat Al Fatihah

idatsikira ku Makkah, ena amati idatsikira ku Madinah Mtumiki

(SAW) atasamuka kuchoka ku Makkah, koma zoona ndi zoti

Surayi idatsikira ku Makkah Mtumiki (SAW) asadasamuke

kupita ku Madinah. Umboni wake ndi Surah 15 (Al Hijr) ndime

87 imene ikunena kuti:

ظ�

ع

ال

قرآن

ال

ثا� و

م

ال

بعا من

آتيناك س

لقد

)87(و

“Ndipo ndithu, takupatsa (Aya izi) zisanu ndi ziwiri

zomawerenga kawirikawiri, (Surat Fatihah), ndi Qur'an

yolemekezeka.”

1 Zimanenedwa kuti Surah imeneyi idatsika pa nthawi imene Mtumiki (SAW) amamva

kuitana kuti: “E! Muhammad.” Mtumiki (SAW) amati akamva mau oyitanawa amachoka pa malopo mofulumira. Munthu wina wotchedwa Warqah adamuwuza Mtumiki (SAW) kuti akamvanso kuitanako akhale tchelu kuti amve zimene oyitanayo akufuna kunena. Pamene adamvanso kuyitanako Mtumiki (SAW) adayankha kuti: “Labbayka!” Kenako mauwo adati: “Nena kuti: Ash-hadu an laa ilaaha illallaahu wa anna Muhammadan rasulullaah. (Ndikuyikira umboni kuti palibe Mulungu wina wachoona koma Allah, ndipo ndithu, Muhammad ndi Mtenga Wake.)” Kenako adati: “Nena: [Alhamdulillahi rabbil ‘aalamin. Al rahmanir rahim.Maliki yawmiddin.]”mpaka adamaliza Surat Al Fatiha.

Page 11: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

11

Ayah zisanu ndi ziwiri (7) zimenezi ndi za mu Surat Al Fatihah.

Surat Al Hijr imene ikukamba za Surat Al Fatihayi idatsikira ku

Makkah, choncho ndizosamveka kuti Surat Al Hijr ikambe za

Surah yoti sidatsike.

Surat Al Fatihah ili ndi mayina ambiri, ena mwa iwo omwe ali

odziwika bwino ndi:-Fatihatul Kitab, Ummul Quran ndi

Assab’ul Mathani.

Fatihatul Kitab: Yotsegulira Buku (la Quran),

imatchedwa chonchi chifukwa ndiyoyambilira mu Buku

la Quran.

Assab’ul Mathani: (Ndime) zisanu ndi ziwiri (7)

zobwerezedwa, imatchedwa chonchi chifukwa ndi ndime

zisanu ndi ziwiri zokhazo zomwe zimabwerezedwa

ndikuwerengedwa kawirikawiri pa Salah.

Ummul Quran: Kholo la Quran, imatchedwa chonchi

pazifukwa zatchulidwa m’mwambazo.

Surayi imatchedwanso kuti Surat Al Hamdu (Yotamanda

Mulungu), Surat Ash-Shifaa (yochiza matenda), Surat As-

Salah (chifukwa chakuti Salah simalandiridwa popanda

kuwerenga Surayi) Mtumiki (SAW) akunena kuti:

“Amene wapemphera Salah ndipo sadawerenge Kholo la Quran

(Al Fatihah) Salatiyo ndiyosakwana”

Mulungu mu Hadith Qudsi akunena kuti:

“Ndayigawa Salah pakati pa Ine ndi kapolo Wanga m’matheka

awiri, ndipo kapolo Wanga apeza zimene apemphe. Kapolo

akanena kuti “Alhamdulillahi rabbil ‘alamin (Kutamandidwa

Page 12: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

12

konse ndi kwa Mulungu Mbuye Wa zolengedwa zonse),”

Mulungu amanena kuti: “Wandiyamika kapolo Wanga.”

(Kapolo) akanena kuti: “Al rahmanir rahim (Wachifundo

chambiri Wachisoni chosatha).” Mulungu amanena kuti:

“Wanditamanda kapolo Wanga.” Akanena kuti: “Maaliki

yuwmiddin (Mwini tsiku la chiweruzo).” Mulungu amati:

“Wandikweza kapolo Wanga.” Akanena kuti: “Iyyaka na’budu

wa iyyaka nasta’in (Inu nokha tikukupembedzani ndiponso Inu

nokha tikukupemphani chithandizo).” Mulungu amati: “Izi ndi

za pakati pa Ine ndi kapolo Wanga ndipo kapolo Wanga apeza

zimene apemphe.” Akanena kuti: “Ihdinas siraatal mustaqim,

siraatalladhina an’amta ‘alayhim, ghayril magh-dhubi

‘alayhim waladh-dhaallin (Tiongolereni ku njira yoongoka.

Njira ya omwe mudawapatsa chisomo, osati ya amene

adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera).”

Mulungu amanena kuti: “Izi ndi za kapolo Wanga ndipo kapolo

Wanga apatsidwa zimene wapempha.”

Tikaonetsetsa bwino mu Hadithiyi Mulungu akuti: “Ndayigawa

Salah”koma imene tamva ikugawidwa ndi Surat Al Fatihah,

chifukwa choti Surayi ndi kholo la Salah, Salah simalandiridwa

popanda kuwerenga Al Fatihah.

Page 13: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

13

NDIME 1

(Ndime Yoyamba)

�سم ن اهللا

ح� الر

)1( الر

Bismillahir Rahmanir Rahim

(1) M'dzina la Mulungu Wachifundo Chambiri, Wachisoni.

Mukatsekula Buku la Quran mupeza kuti kumayambiliro kwa

Surah iliyonse kuli mau amenewa oti: “ �سم ن اهللا

ح� الر

الر

Bismillahir Rahmanir Rahim” kupatula Surat At-Tawbah. Umo

ndi momwe Quran idabvumbulutsidwira.Choncho munthu

ayenera kuyamba ndi mawuwa asadayambe kuwerenga kapena

kulemba ndimeza Buku la Quran.

Mbiri ya Mtumiki Muhammad (SAW) imafotokoza kuti:

M'ngelo Jibril (AS) adawonekera kwa Mtumiki Muhammad

(SAW) panthawi imene iye adali ku phanga lotchedwa Hiraa.

Jibril (a) adati kwa Mtumiki Muhammad (saw): ''Werenga!''

pokhala munthu oti sadaphunzire kulemba kapena kuwerenga,

iye adati ''Ine sinditha kuwerenga.'' Koma pofuna kukwaniritsa

zomwe watumidwa ndi Mulungu, Jibril adamukakamiza

Mtumiki (SAW) kuti awerenge nati: “Werenga”. Munthu

ukawuzidwa kuti “Werenga” ndiye kuti zowerengazo mwina zili

m’mutu udaloweza kapena zalembedwa penapake kuti uzionera

ndikumawerenga. Mulimonsemo, Mtumiki (SAW) zidamuvuta

kuti awerenge chifukwa adalibe zimene adaloweza komanso

Page 14: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

14

ngakhale zikadalembedwa penapake sakadatha kuwerenga

chifukwa iye sadaphunzire kuwerenga, choncho iye Mtumiki

(SAW) adamuwuzanso Jibril (AS) kuti: “Ine sinditha

kuwerenga.” Koma Jibril (AS) atamva kuti iye samatha

kuwerenga adakakamirabe kumuwuza Mtumiki (SAW) kuti:

“Werenga” Ndichifukwa chiyani Jibril (AS) atamva kuti

Mtumiki (SAW) samatha kuwerenga adalimbikirabe kumuwuza

kuti: “Werenga”? Chifukwa chakuti Jibril (AS) amamudziwa

Mulungu kuti ndi Wakutha kupanga chirichonse, choncho

kudali kumuwuza Mtumiki (SAW) kuti iwe Muhammad!

(SAW) ngakhale uli wosatha kuwerenga, koma ngati uwerenge

m’dzina la Mulungu, ukwanitsa kuwerenga. Choncho Jibril

(AS) adamuwuza Mtumiki (SAW) kuti awerenge m’dzina la

Mulungu, adati:

أ

ر

ك باسم اق ب

ي ر )1( خلق ا�

“Werenga!Mdzina la Mbuye Wako yemwe adalenga

(zolengedwa zonse).”[Quran 96:1] mpaka kufikira ndime

yachisanu mu Surayi.

Mau akuti “ �سم ن اهللا

ح� الر

الر Bismillahir rahmanir rahim”

Kumayambiliro kwa Surat Al Fatiha ali ndi nambala (1) pamene

kumayambiliro kwa surah zina zonse mauwaalibe nambala. Izi

zili choncho chifukwa mauwa mu Surah Al Fatiha ndi ndime

yoyamba. Pamene m’ma Surah ena onse mauwa samatengedwa

kuti ndi Ndime (Ayah) kupatula Bismillah amene akupezeka mu

Surah 27 (An Naml) ndime 30:

Page 15: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

15

من إنه

ان

ليم

س إنه

�سم و ن اهللا

ح� الر

)30( الر

“Yachokera kwa Sulaiman, ndipo mawu ake ndi awa: M'dzina

la Mulungu, Wachifundo Chambiri, Wachisoni.”

Ena amati Bismillah mu Surat Al Fatihah sindime yoyamba

ndipo ndime yoyamba mu Surayi ndi “Alhamdulillahi rabbil

‘aalamin”. Kutengera mu Surat Al Hijr kuti ndime 87:“Ndipo

ndithu, takupatsa (Aya izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga

kawirikawiri, (Surat Fatihah), ndi Qur'an yolemekezeka.”Surayi

ndime zake ndi 7, ndipo amene amati Bismillah sindime mu

Surayi amagawa ndime yomaliza mu Surayi pawiri motere:-

اط

صرين ا�

ت

م

ع

م أن ل�

)6(ع

6-Njira ya omwe mudawapatsa chisomo.

ضوب غري

غ

مم ال ل�

ال ع

الني و )7( الض

7-Osati ya amene adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe

adasokera.

Choncho amakwana ma Ayah asanu ndi awiri (7).

Bismillah

“M’dzina la Mulungu”

Bismillah ndi chiganizo chomwe chili ndi mau atatu m'kati mwake.Mau ake ali motere: Bi-Ismi-Allah. Akaphatikizidwa, “I” wa kumayambiliro kwa Ismi, pamodzi ndi “A” wa kumayambiliro kwa Allah amachotsedwa ndipo mawu onse pamodzi amalembedwa motere: Bi-smi-llah (Bismillah) kutanthauza kuti “M’dzina la Mulungu”

Page 16: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

16

Dzina loti: “Allah” ndi la Iye Yekha Wapamwambamwamba, ndipo sikoloredwa kumutcha wina aliyense kapena china chirichonse ndi dzina loti: “Allah”.

Cholinga choyamba kunena kuti “Bismillah – M’dzina la

Mulungu” pochita zinthu ndichani?

Kunena kuti “M’dzina la Mulungu” zimatanthauza kuti

chirichonse chimene tikufuna kupangacho tikuchiyamba

m’dzina la Mulungu. Mwachitsanzo: Ndikuyamba kuwerenga

Quraniyi m’dzina la Mulungu, Ndikuyamba kulemba m’dzina la

Mulungu, Ndikuyamba kudya m’dzina la Mulungu, Ndikutsekula

chitsekochi m’dzina la Mulungu, Ndikuyamba kulankhula

m’dzina la Mulungu, ndi zina zotero.

Cholinga choyamba kuwerenga Quran kapena kuchita chinthu

chirichonse ndi dzina la Mulungu chimakhala kupempha

madalitso kwa Mulungu, chitetezo ndi chithandizo, kuti

Mulungu achitheketse ngati chili chosatheka, achifewetse

kapena kuchiphweketsa ngati chili cholimba kapena chovuta.

Mwachitsanzo ngati tikuwerenga Quran timayamba ndi

Bismillah kuti Mulungu atidalitse poyipanga Quraniyo kuti

ikhazikike m’mitima mwathu, itiwongolere ndikuti ikhale

mankhwala ndi mchizo wa matenda a mumtima komanso

matenda ena aliwonse. Mu Surah 17 (Al Israa) ndime 82,

Mulungu akuti:

ل ننز

وقرآن من

ا ال

م

شفاء هو

ة

ر

منني و

مؤ

ال لل

زيد و

ارا إال الظالمني ي

خس

)82(

Page 17: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

17

“Ndipo tikuitumiza Qur'an yomwe imachiritsa (matenda a m’mitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira...”

Ngati chili chakudya, kuti Mulungu achidalitse, chigwire ntchito yake moyenelera m’thupi ndi kuti ngati chakudyacho chili ndi zoipa monga tizilombo toyambitsa matenda kapena mankhwala monga Poisoni, kuti Mulungu atiteteze ku zoipazo. Ngati ili ntchito kuti Mulungu aipange kukhala yofewa komanso yaphindu ndi zina zotero. Kuwerenga Bismillah kumakhalanso kupempha chitetezo kwa Mulungu kuti atiteteze ku Shaytan (Satana) ndi ma Jini oipa komanso anthu ochita zaufiti (matsenga) ndi ochita nsanje kapena zoipa zina zilizonse. Mtumiki (SAW) adati:

“Ntchito iliyonse yomwe sidayambe ndi Bismillahir rahmanir rahim ndiyopanda madalitso.”

Pomaliza, munthu akazolowera kuyamba chirichonse ndi Bismillah, amakhala woopa kupanga chinthu popanda kuyamba ndi Bismillah, choncho sangapange chinthu choipa chifukwa choipa sangayambe ndi Bismillah.

Dzina loti “Allah” sililoredwa kumutcha wina aliyense koma Mulungu yekha.

Al Rahman Al Rahim

Wachifundo chambiri, Wachisoni (chosatha).

Al Rahman ndi Al Rahim ndi maina awiri m’maina 99 a Mulungu.

Mawu oti Al Rahman ndi Al Rahim amachokera ku liwu loti “Rahmah” kutanthauza kuti Chifundo. Wachifundo

Page 18: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

18

amatchedwa kuti “Raahim”, wachifundo chambiri kapena wachifundo kwambiri amatchedwa kuti “Rahmaan” kapena kuti “Rahiim” amene ali Mulungu Yekha. Kufikira pamenepa tadziwa kuti Al Rahman ndi Al Rahim mawu onse awiri amatanthauza kuti Wachifundo kwambiri, chambiri kapena choposa, chatsala ndichoti tidziwe kusiyana kwa mawu awiriwa.

Ena amati Al Rahman ndiko kuti Mulungu ndi Wachifundo chambiri pa Iye Yekha ngakhale patapanda kupezeka owachitira chifundocho, Iye Mbiri Yake ndiyoti: “Wachifundo Chambiri” Adali Wachifundo wochitiridwa chifundowo asadalengedwe, ndipo ndi Wachifundo komanso adzakhala Wachifundo mpaka muyaya. Kuti zimveke bwino tipereke chitsanzo cha munthu amene wamaliza maphunziro ake a udokotala, yemwe sadayambe kugwira ntchito yake ya udokotala. Ngakhale sadagwireko ntchito ya udokotala, komanso sadachiritseko odwala, timamutchabe kuti Dokotala. Panthawi imeneyi tikumutcha kuti Dokotala chifukwa chakuti ali ndi luso la udokotala, osati chifukwa chakuti amagwira ntchito imeneyi kapena kuti adachiritsako odwala. Chimodzimodzi Mulungu adali “Wachifundo” asadalenge chirichonse. Choncho nthawi zambiri mu Quran timapeza kuti mau oti Al Rahman amatchulidwa pamene Iye (Allah) akufotokoza za Ulemelero Wake, osati pamene akunena zowachitira zabwino akapolo Ake.

Mu Surah 20 (Taha) Allah akufotokoza za Ulemelero Wake kuyambira ndime ya 4:

ن خلق زيال ممع� تن

ات ال

او

م الس

و

رض

ى )4( األ

و

ش است �

� ال

ع

ن

)5( الر

ى

الثر

ت

ا تح

م

ا و

ي�ما ب

م

رض و

ا يف األ

م

ات و

او

م ا يف الس

)6(م

Page 19: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

19

“Chivumbulutso chochokera kwa Yemwe adalenga nthaka ndi thambo lotukuka. (Al Rahman) Wachifundo, pampando wachifumu adakhazikika. Zonse za kumwamba ndi za pansi ndi zapakati pake ndi za pansi panthaka ndi za Iye.”

Mpaka kufikira ndime ya 8 Mulungu akufotokoza za ulemelero Wake. Mwachidule mau oti Al Rahman mu Quran sadatchulidwe molumikizana ndikuwachitira zabwino akapolo ake kapena zolengedwa zake.

Pamene Al Rahim, malo ambiri adatchulidwa motsatizana ndi kuwachitira akapolo ake zabwino. Timubweretsenso dokotala uja, pano wayamba ntchito yake ya udokotala ndipo wachiritsa odwala angapo, nthawi ino timutcha kuti ndi Dokotala osati chifukwa ali ndi luso la udotolo lokha ayi, koma chifukwa amachiritsanso odwala1. Chimodzimodzi Al Rahim ndi Wachifundo chifukwa amachitira zabwino akapolo ake ndi zolengedwa zake zonse. Ndime zambiri zimene muli mau oti Al Rahim zimatsatizana ndikuchitira zabwino akapolo ake.

إن بالناس اهللا

وف

ء

ح� لر

)143( ر

“…Pakuti Mulungu ndi Woleza kwabasi kwa anthu, (Rahim) ndi Wachifundo chambiri.” [Quran 2:143].

Mu Surah 16 (An Nahl) ndime 5 mpaka 8, Mulungu akufotokoza za chifundo chake pa anthu, mu ndime ya 7 akunena za zabwino zimene adatichitira podzichepetsa

1Timakhulupilira kuti amene amachiritsa ndi Mulungu ndipo dokotala komanso

mankhwala ndinjira imene Mulungu amachiritsira odwala.

Page 20: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

20

mphamvu ziweto kuti tithe kudzigwiritsa ntchito mosavuta, ndipo akuti:

مل

تح

قال�م و

� إ� أث الغيه تكونوا لم ب

فس �شق إال ب

ن

ب�م إن األ

ر

وفء

لر

ح�

)7( ر

“Ndipo zimasenza mitolo yanu (yolemera) kukafika nayo ku midzi yakutali komwe simumatha kukafikako popanda kuvutika kwambiri. Ndithu Mbuye wanu ndiwodekha kwambiri, (Rahim) ndiwachisoni.”

Ndime ngati zimenezi ndi zambiri mu Quran, mwachidule, Al Rahman ndi Wachifundo pa Iye Yekha mu Ulumelero Wake, pamene Al Rahim ndi Wachifundo powachitira zabwino akapolo kapena zolengedwa zake zonse.

Ena amati Al Rahman ndi Wachifundo ndipo chifundo chake amachitira akapolo Ake onse okhulupilira ndi osakhulupilira omwe mu umoyo uno. Mulungu amadyetsa wina aliyense, amagwetsa mvula kwa wina aliyense amachita zabwino zambiri kwa wina aliyense posayang’ana kuti ndiokhulupilira kapena osakhulupilira chifukwa onse ndi zolengedwa zake ndipo Iye yekha ndi amene ali ndi udindo woziyanga’nira. Iye Mulungu ndi Mlengi, Mbuye wa aliyense choncho chifundo chake amapereka kwa wina aliyense.

Pemene Al Rahim ndi Wachifundo kwa okhulupilira okha mu umoyo umene uli nkudza, chifukwa osakhulupilira ndiothamangitsidwa m’chifundo cha Allah mu umoyo umene uli nkudza ndipo malo awo ndi ku moto. Tikumati Al Rahman ndi “Wachifundo chambiri” chifukwa chifundo chake ndi chambiri

Page 21: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

21

chimampeza aliyense, Al Rahim “Wachisoni chosatha” chifukwa chifundo Chake ngakhale chidzakhale kwa anthu ochepa (okhulupilira okha) koma chidzakhala chosatha mpaka muyaya. Choncho ma Sheikh ena amamasulira kuti: “Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.”

Pomaliza, “Al Rahmanir Rahim” Iye ndi Wachifundo pa Iye Yekha, chifundo Chake mu umoyo uno chimamupeza wina aliyense wokhulupilira ndi wosakhulupilira yemwe, ndipo umoyo uli nkudza chidzakhala kwa okhulupilira okha.

*******

Page 22: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

22

NDIME 2

(Ndime Yachiwiri)

د

م

ح ال ب هللا

المني ر

ع

)2( ال

Alhamdulillahi rabbil ‘aalamin

(2) Kutamandidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye Wa

zolengedwa zonse.

Pambuyo poti Mulungu watiphunzitsa kuti tidziyamba zinthu za

umoyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndi Bismillah, akupitiriza

kutiphunzitsanso m’mene tingamutamandire. Mulungu

akadangoti “Mutamandeni Mbuye wanu” zikadativuta kuti

tibweretse mau abwino ndi oyenera kumutamandira Iye,

aliyense akadabweretsa mawu ake molingana ndi nzeru zake.

Koma Mulungu adatichitira chifundo potiphunzitsa kuti

tidzimutamanda Iye ponena kuti: “Alhamdulillah rabbil

‘alamin.”

Tanthauzo la: “Alhamdulillahi rabbil ‘alamin”

Alhamdu: Kutamandidwa (konse), Lillahi: Ndi kwa Mulungu,

Rabbi: Mbuye (wa), Al ‘alamin: Zolengedwa zonse.

Alhamdulillah

Mau akuti Alhamdulillah amatanthauza kuti: "Kutamandidwa

konse ndi kwa Mulungu." Mauwa amatanthauzanso kuti:

"Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu."Kusiyana kwa

Kutamanda ndi Kuyamika kuli motere:-

Page 23: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

23

Kutamanda kumakhala m’kulankhula, umamutamanda

munthu ndi mawu osati ndi zichitochito, pamene

Kuyamika (kumatchedwanso kuti Kuthokoza),

kumatheka ndi mawu komanso ndi zichitochito.

Ukamuona munthu wa mphamvu umamutamanda

polankhula kuti: “Amene uja ndi wamphamvu.” Pamene

yemwe wakupatsa malaya, umamuyamika polankhula

kuti: “Zikomo kwambiri” komanso umaonetsa kuyamika

powagwiritsa ntchito malayawo.

Timamutamanda Mulungu chifukwa cha Ulemelero

umene ali nawo komanso chifukwa cha zimene

amatichitira. Pamene Kuyamika, timamuyamika Iye

(Mulungu) chifukwa cha zimene amatichitira osati

chifukwa cha Ulemelero Wake.

Ngakhale mawu awiriwa akumveka kuti ndiosiyana,

sizolakwika kutanthauzira “Alhamdulillah” kuti: Kuyamikidwa

konse ndi kwa Mulungu, chifukwa mau oti: “Alhamdu”

tikamakamba za Mulungu amatanthauza zonse ziwiri

(Matamando komanso Mayamiko), koma mau amene ali

oyandikira kwambiri ndi “Kutamandidwa”. Pamene

Kuyamika/Kuthokoza mu Chiarabu ndi Shukr. Choncho

tikaonetsetsa mu Quran tipeza kuti mau oti: “Alhamdulillah”

agwiritsidwa ntchito pamene Mulungu akukamba za Ulemelero

Wake komanso pamene akukamba za zabwino zomwe

amawachitira akapolo Ake.

Zitsanzo za “Alhamdu” (kutamanda ndikuthokoza):

Page 24: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

24

Kutamanda: Mu Surah 34 (Saba) ndime yoyamba,

Mulungu akufotokoza za Ulemelero Wake, zimene ali

nazo ndi zimene amachita, sakufotokoza zowachitira

akapolo Ake zabwino ndipo wagwiritsa ntchito mau oti:

“Alhamdulillah”:

د

م

ح ال ي هللا ا�

ا �

ات يف م

او

م ا الس

م

رض يف و

األ

د و

م

ح

ة يف ال

خر

اآل

هو

و

ك�

ح

ال

خبري)1( ال

“Kuyamikidwa (Alhamdu) kwaulemu ndi kwa Mulungu

Yemwe zakumwamba ndi zapansi ndi zake.Ndipo

kutamandidwa konse kwaulemu pa tsiku lomaliza ndi

Kwake. ndiponso Iye ndiwanzeru zakuya, ndiwodziwa

chirichonse.”

Kuyamika/Kuthokoza: Pamene M’neneri Ibrahim (AS)

adachitiridwa zabwino ndi Mulungu popatsidwa ana iye

ali wokalamba kwambiri adathokoza Mulungu, ndipo

Quran pa nkhaniyi yagwiritsa ntchito mau oti

“Alhamdulillah” kutathauza kuthokoza:

د

م

ح ال ي هللا ا�

هب

� � و

�رب ع

اعيل ال

اق إ�

إسح

� إن و

ر

ميع

اء لس

ا�ع

)39(

“Kuyamikidwa (Alhamdu) konse ndi kwa Mulungu

Yemwe wandipatsa ine kuukulu Ismail ndi Isihaka.

Ndithu, Mbuye wanga ndiwakumva pempho (la kapolo

Wake).”[Quran 14 (Ibrahim) ndime 39]

Pamene mau oti “Shukr” amatanthauza Kuthokoza kokha

pachimene wachitiridwa ndipo adagwiritsidwa ntchito mu

Quran malo okhawo amene Mulungu amakamba zowachitira

Page 25: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

25

zabwino akapolo Ake. Mu Surah 40 (Ghaafir) ndime 61

Mulungu akuti:

ي اهللا ل ا�

ع

ج

فيه ل�سكنوا الليل ل�م

ار

ال�

بصرا و إن م

ل �و اهللا

� فض

الناس ع

ل�ن

و

ثر

ال الناس أك

ون

كر

)61( �ش

“Mulungu ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti mupumule

mmenemo, ndi usana kukhala wounika (kuti muthe kuchita

ntchito zanu). Ndithu, Mulungu ndi Mwini kupereka ufulu kwa

anthu. Koma anthu ambiri sathokoza.”

Ayah zonga izi zilipo zambiri mu Quran. Choncho Alhamdu ndi

kutamanda komanso kuthokoza, pomwe Al shukr ndi kuthokoza

kokha. Tiyenera kumuthokoza Mulungu Yemwe wakupanga

kumuthokoza Iye m’mawu ochepa oti: “Alhamdulillah” ndipo

kwa Iye mau amenewa amakwana. Alhamdulillah!

Zikunenedwa kuti kutamandidwa/kuyamikidwa "konse" ndi

kwa Iye Allah, chifukwa pamene tikumutamanda munthu

chifukwa champhamvu zake, kumakhala kumutamandanso

amene adapereka mphamvuzo Yemwe ndi Mulungu.

Tikamayamikira kukoma kwa chakudya, mayamikowo amapita

kwa amene waphikachakudyacho komanso kwa amene

adapereka luso lophika Yemwe ndi Mulungu. Palibe chimene

munthu angachite pokhapokha chimene Mulungu waloleza kuti

achite, matamando onse ndi mayamiko kothera kwake ndi kwa

Iye Allah. Choncho, Kutamandidwa ndi Kuyamikidwa kooonse!

ndi kwa Mulungu, Mbuye Wa zolengedwa zonse.

Rabbil ‘alamin

Page 26: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

26

“Mbuye Wa zolengedwa zonse”

Tikaiwonetsetsa kwambiri ndime imeneyi tipeza luntha ndi

kuzama kwa mawu a Mulungu. Mau ena aliwonse mu Quran ali

pa malo pake poyenelera komanso mochititsa chidwi. Mulungu

adafuna kuti Surat Al Fatihah ikhale kumayambiliro kwa Quran

chifukwa cha zomwe Surayi yatenga. Mabuku ambiri timapeza

“MAU OYAMBAkomanso “ZA M’KATIMU” timapeza kuti

mwalembedwa zokhudza mwini buku mwachidule kwambiri,

mbiri zake, maphuziro ake ndi zina zotero. Ena amalembanso

pemphero kuti cholinga cha bukulo chikwaniritsidwe, komanso

amalemba mwachidule zomwe zikupezeka m'kati mwa bukulo.

Quran idayambanso chimodzimodzi, pambuyo pa matamando,

ikufotokoza mwachidule za Mwini Bukuli (Quran) kuti Iye ndi:

“Mbuye Wa zolengedwa zonse. Wachifundo chambiri,

Wachisoni.Mwini tsiku la chiweruzo.”Ikupitiriza kunena kuti

Iye ndi Yemwe aliwoyenera kumupembedza komanso

kumupempha chithandizo: “Inu nokha tikukupembedzani

ndiponso Inu nokha tikukupemphani chithandizo.” Komanso

ikupitiriza ndi pemphero kuti cholinga cha Bukuli chomwe ndi

Chiwongoko chikwaniritsike: “Tiongolereni ku njira yoongoka.

Njirayaomwe mudawapatsa chisomo; osati ya amene

adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera.”

Tikapitiriza kuwerenga Surah yotsatirayo, Surah 2 (Al Baqara)

ndime 2, yatibweretsera “Za m’katimu” za Buku limeneli: “Ili

ndi Buku lopanda chipeneko mkati mwake; Ndi chiongoko cha

(anthu) oopa Mulungu.” Ndizoloredwanso kuwerenga motere:

Page 27: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

27

“Ili ndi Buku lopanda chipeneko.Mkati mwake (muli) chiongoko

cha (anthu) oopa Mulungu.”Za m’kati mwa Buku limeneli ndi

chiongoko kwa oopa Mulungu.

Zikutanthauzanji Quran ikamati “Mbuye Wa zolengedwa

zonse”? Sindife oyamba kufunsa funso limeneli, Farawo

adafunsa Mneneri Musa (AS) funso longa lomweli, ife tikufunsa

ndicholinga chofuna kuphunzira, pamene Farawo kudali

kudzikweza kuti ndaninso mbuye wosakhala iye Farawo. Timve

kuchokera kwa Musa (AS), Surah 26 (Ash Shu’araa) ndime 23

ndi 24:

المني

عب ال

ا ر

م

و

ون

ب )23( قال فرع

� قال ر

كن

ا إن

ي�م

ا ب

م

رض و

األ

ات و

او

م الس

وقنني )24( م

“Farawo adati: ‘Kodi ndani Mbuye wazolengedwayo?’ (Musa) adati: ‘Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli ndi chitsimikizo.”

Ndimeyi yafotokoza mwachimvekere kuti zolengedwa zonse ndi kuyambira ntambo wakumwamba, dziko la pansi ndi zonse zomwe zikupezeka m'menemo ndi pakati pa ziwirizi. Mbuye wa zonsezi ndi Mulungu

“Rabb”(Mbuye) kuchokera pa Rabbil ‘alamin,mau amenewa ali ndi matanthauzo angapo ena mwa iwo ndi: Mwini, Mbuye, Mleri ndi Bwana. Matanthuzo onsewa akusonkhana m’mau oti: Mbuye.

Rabb: Mbuye, Mwini ndi Mleri (amene amayang’anira zolengedwa zake zonse).

Page 28: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

28

Al ‘alamin “Zolengedwa zonse.” Chopezeka chirichonse, kupatula Iye Mwini, (chimene chidapezekako, chikupezeka ndi chimene chadzapezeka) ndicholengedwa cha Mulungu. Kulingalira mozama m'zolengedwa za Mulungu kumabweretsa Imaan ndi kuopa Mulungu (Taqwa). Zolengedwa za Mulungu ndi zambiri kotero kuti tikulephera kuzisimba pogwiritsa ntchito mawu kapena zilembo koma tingoti: Atamandike Mbuye wathu! Yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake ndikuchiongolera!

Tikamati Mulungu amayang’anira, kuyang’anira Kwake sikuli ngati momwe ife timayang’anira zinthu zathu. Tikatembenukira kumbali sitidziwa chomwe chikuchitika kumbuyo, timagona osadziwa chomwe chikuchitika, pamene tikusamalira chinthu chimodzi zina timakhala tazisiya kapena kuyiwala kumene, pamene Mulungu nthawi zonse palibe chimene chimamudutsa, amadziwa, amamva ndi kuona zonse nthawi zonse.

ال ...

ب

ز

ع ي ه

ن

قال ع

ة مث ات يف ذر

او

م ال الس

رض يف و

ال األ

و

ال ذلك من أص�

و

رب

اب يف إال أكبني كت

)3( م

“…Sichingabisike kwa Iye cholemera ngati njere; chakumwamba, chapansi ngakhale chochepa kuposa chimenecho; ngakhale chokulirapo, koma (zonsezo) zili m'Buku (Lake) losonyeza poyera (chirichonse).” [Quran 34 (Saba) ndime 3] Tulo sitimamupeza ndipo samasinza, kuti Iye kumupeze kusinza, kumwamba, pansi ndi zonse zomwe zili m’kati mwa ziwirizi ndi pakati pake zikhoza kuonongeka komanso kutha.

ال اهللا

إال إ�

هو �

ال

قيوم

ال ال

خذه

تأ

ال سنة

نوم و

ا �

ات يف م

او

م ا الس

م

يف و

رض

)255(... األ

Page 29: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

29

“Mulungu palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo Wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chirichonse.Kusinza sikumgwira ngakhale tulo.zonse zakumwamba ndi zapansi ndi za Iye.” [Quran 2 (Al Baqara) ndime 255]

Alemekezeke Mulungu! Mbuye wa zolengedwa zonse!

*******

Page 30: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

30

NDIME 3

(Ndime Yachitatu)

ن

ح� الر

)3( الر

Al Rahmanir Rahim

(3) Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.

Mu ndime yathayi, Mulungu amatiuza za Mbiri Yake kuti Iye ndi Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mu ndime ino akupitiriza kutchula zina mwa mbiri Zake kuti Mulungu Amene kutamandidwa konse ndi kwake, ndi Mbuye Wazolengedwa zonse komanso ndi Wachifundo chambiri ndi chisoni chosatha.Tafotokoza kale tanthauzo la Al Rahman Al Rahim (Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha) mu ndime yoyamba mu Surayi, choncho sitibwereza mu ndime imeneyi, tipita ndime yotsatirayo yomwe Mulungu akupitirizabe kutiuza Mbiri Zake.

*******

Page 31: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

31

NDIME 4

(Ndime Yachinayi)

الك

ين م وما�)4( ي

Maaliki yawmiddin.

(4) Mwini tsiku la chiweruzo.

Ndime imeneyi ili ndi kawerengedwe kosiyanasiyanamonga:

ين وم ا�الك ي

ين Maaliki yawmiddin” komanso“ م وم ا�

لك ي

Maliki“م

yawmiddin.” Kusiyana kwake ndikoti kawerengedwe

koyambako timakoka mau oti Maalik, pamene kawerengedwe

kachiwiriko ndi Malik. Tikawerenga mokoka tanthauzo

limakhala: Mwini tsiku la chiweruzo, tikapanda kukoka

tanthauzo limakhala: Mfumu ya tsiku lachiweruzo, matanthauzo

onse awiri ndiolondola. Ena amawerenganso kuti ل

وم يمك ي

ين ”.Maliiki yawmiddin“ا�

Mulungu mu ndime imeneyi akutiuza kuti Iye ndi Mfumu

komanso Mwini tsiku la chiweruzo. Ngati Allah ali Mwini

komanso Mfumu ya tsiku lachiweruzo, nanga masiku enawa

mwini komanso mfumu ndi ndani

Tsiku ndinthawi, Mulungu adalenga chirichonse

kuphatikizaponso nthawi, nthawi ndi cholengedwa cha

Mulungu, choncho masiku onse ndiolengedwa ndi Mulungu.

Page 32: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

32

Mulungu ndi Mwini masiku onse. Ngati Iye ndiye Mwini

masiku onse, ndichifukwa chiyani wapatula tsiku limeneli kuti

ndi tsiku lake pamene masiku onse Mwini ndi Iye?

Munthu, pa dziko lapansi, adapatsidwa gawo la ufulu ndi

mphamvu zotha kuchita chimene akufuna.Akhoza kuyima,

kugona, kuyenda, kuthamanga ndi zina zambiri m’mene iye

akufunira. Mulungu akamulamula kuti asadye nkhumba, iye

(munthu) alindi mphamvu zomwe adapatsidwa ndi Mulungu

zotha kusiya osadya nkhumbayo kapena kudya, akhoza

kulankhula kapena kukhala chete pamene wafuna.Aka ndi

kagawo kochepa ka ufulu ndi kudzilamulira kamene munthu

adapatsidwa m’masiku a umoyo uno. Pamene likadzafika tsiku

la chiweruzo, ufulu ndi mphamvu zimenezi zidzalandidwa ndipo

sadzatha kuchita chinthu chomwe iye akufuna ngati momwe

amachitira m’masiku a pa dziko. Umwini wotha kudzilamulira

udzatha ndipo udzatsala Umwini wa Mulungu. Choncho Mwini

Wachirichonse pa tsikuli ndi Mulungu.

Chimodzimodzi tikatanthauzira kuti “Mfumu ya tsiku

lachiweruzo,” Mulungu padziko lapansi amaperekanso gawo

lochepa la ufumu kwa anthu. Amapereka kwa aliyense yemwe

Iye wamufuna, okhulupilira kapena osakhulupilira, wabwino

kapena woipa. Mu Surah 3 (Ali ‘Imran) ndime 26 Mulungu

akuti:

قل الك الل�

ك ممل

� ال

ك تؤ

مل

ن ال

م

زع �شاء

تن

ك و

مل

ن ال مم

تعز �شاء

ن و

م

تذل �شاء

ن و

م

دك �شاء

بي

خري

� إنك ال

ء كل ع )26( قدير �

Page 33: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

33

‘Nena "O! Mbuye wanga! Mwini Ufumu wonse. Mumapereka

ufumu kwa yemwe mwamufuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa

yemwe mwamufuna. mumapereka ulemelero kwa yemwe

mwamufuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamufuna.

Ubwino wonse uli m'manja mwanu.Ndithudi, Inu ndinu

Wokhoza chirichonse.’

Choncho Mulungu amapereka ufumu pa dziko la pansi kwa

amene Iye wamufuna. Tikamati ufumu tikuyambira ufumu wa

m’mudzi, utsogoleri wa gulu la anthu kapena bungwe,

utsogoleri wa dziko ndi utsogoleri wina uliwonse. Mfumu

kapena mtsogoleri amalamulira anthu ake ndipo chonena chake

chimachitika molingana ndi mphamvu zomwe wapatsidwa ndi

Mulungu, ndipo ulamuliro wake ukhoza kukhala wachilungamo

kapena wopondereza. Ufumu wonsewu ndi m’masiku a umoyo

uno. Pamene pa tsiku la chiweruzo ufumu wonse mwa anthu

udzakhala utalandidwa, ndipo udzatsala Ufumu wa Allah.

وم

� ي

ارزون

فى ال ب

خ

� ي

ع م اهللا

ء م� ن �

ك لم

مل

ال

وم

ي

ال احد هللا

و

ار ال قه

ال

)16(

“Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Mulungu). Ndipo palibe chirichonse chidzabisidwa kwa Mulungu (mzinthu zawo). (Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa):"Kodi Ufumu ndiwayani lero? Ndi wa Mulungu m’modzi Yekha, Wopambana, (woweruza mmene akufunira kwa anthu Ake).”[Quran 40 (Ghaafir) ndime 16]

Mu Surah 25 (Al Furqan) ndime 26 Mulungu akunenanso kuti:

Page 34: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

34

ك مل

�ذ ال

وم

ق ي

ح

ن ال

للر

كان

وما و

� ي

ع

�افرين

سريا ال

)26( ع

“Tsiku limenelo ufumu wachoonadi ndi wa (Mulungu)

Wachifundo chambiri. Ndipo lidzakhala tsiku lovuta kwa

osakhulupilira.”

Mulungu ndi Mfumu ya masiku onse, ndipo masiku a umoyo

uno Mulungu amamupatsa amene wamufuna gawo lochepa

kwambiri la ufumu, koma pa tsiku la chiweruzo ma ufumu onse

adzatha udzatsala Ufumu wa Mulungu Yekha, Iye ndi Mwini

komanso Mfumu wa tsikuli.

ين وم ا� ي

Yawmiddin (Tsiku la chiweruzo)

Tsiku, mulingo wake ndiwosiyanasiyana, nthawi zina tikati

tsiku timatanthauza kuyambira kutuluka kwa dzuwa mpaka

kulowa kwa dzuwa, dzuwa likatuluka timati tsiku taliyamba

bwino, likamalowa timati talimaliza bwino. Nthawi zina tsiku

timatanthauza usana ndi usiku. Koma nthawi zambiri tsiku ndi

ma ola makumi awiri ndi anayi (24 hours). Ngakhale nthawi

zambiri tikati tsiku timatanthauza “24 hours” koma mau oti

tsiku amagwiritsidwa ntchito potanthauza nthawi yokwana ma

ola 24, yochepera pamenepo kapena yoposera pamenepo.

Tikawerenga Hadith ya Dajjaal, imati Dajjaal adzakhala pa

dziko pano masiku makumi anayi (40) ndipo tsiku loyamba

lidzakhala lotalika ngati chaka chimodzi, tsiku lachiwiri

lidzakhala lotalika ngati mwezi, tsiku lachitatu

Page 35: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

35

lidzakhalalotalika ngati sabata, ndipo masiku otsalawo

adzakhala otalika mofanana ndi masiku athu (ma ola 24), koma

onsewa akutchedwa kuti masiku ngakhale mulingo wake uli

wosiyana. Mulungu ndi Wakutha kupanga tsiku kukhala ma ola

24, kuchepera pamenepo kapena kuposera pamenepo. Mu Surah

22 (Al Hajj) ndime 47 Allah akunena kuti:

جلونك

ع�ست

ذاب و

ع

لن بال

لف و

خ

ي

اهللا

ده

ع

إن و

وما ود ي

ك عن ب

ف رنة كأل

ا س مم

ون )47( تعد

“Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango.Komatu

Mulungu sadzaswa lonjezo Lake.Ndipo ndithu, tsiku limodzi

kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi (1000) chimodzi

mukawerengedwe kanu.”

Mu ndimeyi Mulungu akutiwuza za tsiku lomwe kutalika kwake

ndikofanana ndi zaka 1000 za ife.

Mu Surah 70 (Al Ma’arij) ndime 4 akukamba za tsiku lina

lomwe kutalika kwake ndikokwana zaka 50 000 kuwerengera

zaka za ife:

ت�

ج ال�كة

م

ال

وح

الر

وم يف إليه و

ي

كان

ه

دار

ف �سني مق

نة أل

)4( س

“Angelo ndi Jibril amakwera kwa Iye (Mulungu) m'tsiku lomwe

kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu (50 000).”

Choncho tsiku simaola 24 okha kapena usiku ndi usana wokha.

Zimanenedwa kuti tsiku la chiweruzo lidzatalika ngati zaka

50000, zomwe zili zodziwika bwino ndi zoti tsikuli likatalika

Page 36: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

36

molingana ndi ntchito za munthu. Likakhala lalifupikwa anthu

ochita zabwino, aliyense molingana ndi ntchito zake, ndipo

likakhala lalitali kwa ochita zoipa aliyense molingananso ndi

ntchito zake. Mwina ndikumafunsa kuti ndizotheka bwanji tsiku

limodzi kukhala lalitali kwa wina ndi lalifupi kwa wina.

Choyamba, ngati ochititsa zimenezo ndi Mulungu ndiye kuti

ndizotheka, Iye ndiwakutha kupanga chirichonse. Izo ndiye

Mphamvu za Mulungu, akhonza kupanga tsiku limodzi kukhala

lalitali kwa ena ndi lalifupi kwa ena, akhonzanso kupanga

masiku osiyana mulingo kukhala otalika mofanana. Chitsanzo

chake ndi cha anthu a m’manda, amene adamwalira kale, amene

akumwalira tsopano ndi amene adzamwalire mtsogolo muno

onse m’manda nthawi yawo ndiyofanana palibe amakhala

m’manda nthawi yaitali kapena yaifupi kuposa nzake.

Ikadakhala nthawi yawo ndiyosiyana ndiye kuti chilango cha

m’manda kwaamene adamwalira kale chikadakhala chochuluka

kuposa amene adzamwalire Qiyama itatsala pang’ono, koma

sizili choncho, aliyense chilango chake ndicholingana ndi

ntchito zake. Umboni komanso chitsanzo chachikulu choti

Mulungu ndi wakutha kupanga tsiku limodzi kukhala lalitali

kwa ena ndi lalifupi kwa ena, komanso kupanga masiku ambiri

ndi ochepa kukhala otalika mofanana, tiwerenge ndime izi:

Surah 2 (Al Baqara) ndime 259 ndi ndime zingapo mu Surah 18

(Al Kahf).

Mu Surat Al Kahf, Mulungu akufotokozankhani ya anyamata

amene adathawira kuphanga ndipo Mulungu adawagonetsa tulo

Page 37: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

37

kwa zaka zoposa ma zana atatu (300). M’ndime ya 11 mu

Surayi Mulungu akuti:

بنا

� فضر

م ع ف يف آذا�

�هددا سنني ال

)11( ع

“Tidawagonthetsa makutu awo, (ndikugona kosamva nako

kanthu) kwa zaka zambirimbiri m'phanga”.

M’ndime ya 25 mu Surayi Mulungu akutiwuza nambala ya zaka

zomwe iwo adakhala ali chigonere m’phangamo:

لبثوا

يف وف�

وا سنني مائة ثالث كه

اد

د

از

)25( �سعا و

“Ndipo adakhala m'phanga lawolo (ali mtulo) zaka

mazanaatatu (300) ndikuonjezera zisanu ndi zinayi (9).”

Adali chigonere kwa zaka 309, koma pamene Mulungu

adawadzutsa, iwo adawona ngati agona tsiku limodzi kapena

gawo chabe la tsiku, mu ndime 19 Mulungu akunena kuti:

كذلك

ا� ون

ث

ع

لوا ب

اء

�س

ي�م لي

قال ب

م قا�ل

� كم م�

ا قالوا لبث

ن

وما لبث

ض أو ي

ع

وم ب

ي

ب�م قالوا

ر

لم

ا أع

� بم )19(...لبث

“Ndipo momwemonso tidawaukitsa kuti afunsane pakati pawo

(zanthawi imene akhala alichigonere). Adanena wonena mwa

iwo: "Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?" Adati,

"Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku." (ena) adati:

"Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala.”

Alemekezeke Mulungu! Amene adapanga nthawi yokwana

zaka 309 kukhala yochepa kwambiri ngati tsiku limodzi lokha,

Page 38: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

38

kapena maola ochepa chabe kwa “Eni Phanga” (As’haabul

Kahf).

Mu Surah 2 (Al Baqara) ndime 259, Mulungu akufotokoza za

munthu yemwe adali ndi bulu wake komanso chakudya cha pa

ulendo, ndipo pamene amadutsa pa mudzi wina umene anthu

ake adamwalira ndipo udagumuka-gumuka,iye adadzifunsa

yekha kuti “Mulungu adzawudzutsa bwanji mudziwu ndi anthu

ake?

ي أو كا�

ر

� م

ة ع قري

هي

و

ة

� خاوي

وشها ع

يي أ� قال �

ح

هذه ي

د اهللا

عا ب

و�

م اته

فأم

ام مائة اهللا

ع

� ثه

ع

كم قال ب

ت

ت قال لبث

وما لبث

ض أو ي

ع

وم ب

قال ي

ل

ب

ت

ام مائة لبث

ع

ظر امك إ� فان

ابك طع

شر

لم و

نه

�س

ظر ي

ان

ارك إ� و

لك �

ع

لنج

ة وظر للناس آي

ان

إ� و

عظام ها كيف ال

شز

ن�

وها �

س

ما نك

ا لح فلم ني

تب

قال �

لم

أن أع

� اهللا

ء كل ع قدير �

)259(

“Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi

umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu)

adati: "Kodi Mulungu adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo

pakufa kwake?" Ndipo Mulungu adampatsa imfa kwanthawi

yokwana zaka zana limodzi (100), kenako adamuukitsa

namufunsa: "Kodi wakhala nyengo yotani?" Adati: "Ndakhala

nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku." (Mulungu) adati:

"Koma wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona chakudya chako

ndi zakumwa zako, sizidaonongeke (sizidavunde). Ndipo

yang'ana bulu wako (ali mafupa okhaokha oyoyoka);ndi kuti

ukhale chisonyezo kwa anthu, (nchifukwa chake takuukitsa ku

Page 39: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

39

imfa). Ndipo yang'ana mafupa(abulu wako) momwe

tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu." choncho pamene

zidazindikirika (kwa iye, woukitsidwayo), adati: "Ndikudziwa

kuti Mulungu Ngokhoza chirichonse."

Poyankha funso la munthuyu, Mulungu adamuchotsa mzimu1

ndipo adali chimwalilire kwa zaka zana limodzi (100),

zachidziwikire kuti thupi lake lidali litasanduka dothi.

Atawukitsidwa ndikufunsidwa za nthawi yomwe wakhala ali

chimwalilire, iye adati wakhala tsiku limodzi kapena gawo la

tsiku. Pamene adayang’ana chakudya chake adachipeza kuti

chili bwino bwino, sichidawole chifukwa chakuti chakudyacho

sichidakhale nawo zaka 100. Pamene adayang’ana bulu wake

adapeza mafupa okha okha kusonyeza kuti buluyo adakhala

zaka 100 zimene iye adali chimwalilire. Mulungu ndiwakutha

kupanga nthawi imodzi kukhala zaka 100 ngati momwe

adachitira kwa buluyo komanso nthawi yomweyo kukhala tsiku

limodzi ngati momwe adachitira ku chakudya cha munthuyu.

1Sheikh Khalid Ibrahim potanthauzira ndime imeneyi akuti “Ndipo Mulungu

adampatsa imfa” sadagwiritse ntchito mau oti “adamupha” chifukwa kupha ndikulichita thupi chinachake kufikira kufa, monga kumenya kapena kuvulaza mpaka kufa, kapena kumudyetsa munthu mankhwala ngati poisoni mpaka kufa, zonsezi umalichita thupi kenaka nzimu umachoka, timati: waphedwa, poisoni wamupha ndi zina zotero, kumeneko kumatchedwa kupha, pa chiarabu amati “ قتل Qatala”. Pamene Mulungu akamakamba za Iye kuchotsa moyo mwa munthu kapena china chirichonse amati “ أمات Amaata” chifukwa “Amaata” ndikuchotsa mzimu popanda kuchita chirichonse ku thupi, amene angathe zimenezo ndi Mulungu Yekha, pamene anthu amangolimbana ndi thupi pofuna kuchotsa moyo wa munthu. Chifukwa choti mau oti: Amaata kuchichewa kulibe, Sheikhewa adamasulira kuti: “Adampatsa imfa”.

Page 40: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

40

Choncho tikamva kuti tsiku la chiweruzo ndilalitali ngati zaka

50000, zisatikayikitse. Tikamvanso kuti tsikuli likatalika

molingana ndi ntchito za anthu tisakayikirenso chifukwa Allah

wationetsa kale kuti Iye ndiwakutha chirichonse.

Mu umoyo wathu watsiku ndi tsiku, zimachitikanso kuti tsiku

lomwelo kwa wina limaoneka kutalika chifukwa cha ziphinjo

zimene munthu akukumana nazo, komanso limaoneka kufupika

kwa amene ali pachisangalalo patsikulo.

Dini

Mau oti Dini, ambiri timagwiritsa ntchito pafupifupi tsiku

lirilonse pofuna kunena za Dini yathu ya chisilamu.

Tikamawerenga ndime imeneyi kumapetoko kulinso mau

amenewa: ين وم ا�الك ي

Maaliki yawmid-din”. Mauwa ndi“ م

amodzi koma ali ndi matanthauza angapo, amatanthauza

“Chipembedzo,” “Chikhulupiliro” komanso “Chiwerengero ndi

Malipiro”. Mu Surah 3 (Aali ‘Imran) ndime 19 mau amenewa

atchulidwanso kutanthauza Chipembedzo:

إن ين د ا�

عن اهللا

سالم

)19(...اإل

Innad-dina ‘inda-llahil islam

“Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Mulungu ndi Chisilamu”

Ndime zomwe mau amenewa atchulidwa potanthauza

chipembedzo zilipo zambiri.

Page 41: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

41

Mu Surah 2 (Al Baqarah) ndime 256, mau oti Din

atchulidwanso potanthauza Chikhulupiliro kapena kuti kulowa

m’chipembedzo:

اه

ر

ين يف ال إك )256...(ا�

“Palibe kukakamiza (munthu kulowa) M'chipembedzo1…”

Mu ndime imene tiriyi mau oti Din sakutanthauza chipembedzo,

sitinganene kuti: Maaliki yawmiddin “Mwini tsiku la

chipembedzo”. Koma akutanthauza “Malipiro”. Tikawerenga

Surah 51 (Adh Dhaariyaat) ndime 6 tipeza kuti mau amenewa

agwiritsidwa ntchito ndipo akutanthauza kuti Malipiro:

إن

وين اقع ا�

)6( لو

“Ndipo, ndithu, malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi.”

1 Tipezerepo mwayi, ndime imeneyi ena samayimvetsetsa bwino; amatanthauzira

molakwika kuti: M’chipembedzo mulibe kukakamizana, choncho munthu akhoza kupanga chimene akufuna kapena kusapanga chimene sakufuna, akhoza kusiya kupemphera, osavala Hijaab chifukwa palibe kukakamizana, kumeneko ndikumva molakwika. Odana ndi Chisilamu amapezeranso mwayi ndipo amafunsa kuti ngati m’chipembedzo mulibe kukakamizana nanga ndi chifukwa chiani munthu akatuluka Chisilamu amaphedwa, kumeneko sikukakamizana? Tiwauze anthu ngati amenewa kuti ndimeyi ikutanthauza kulowa m’chisilamu samakakamizana, koma ukalowa ndiye kuti ukuvomereza malamulo ake onse, choncho udzayenera kutsatira, ngati waphwanya lamulo udzayenera kupatsidwa chilango. Tiwachenjeze achinyamata amene akuphunzira chiarabu kuti kudziwa chiarabu sindiye kuti ungamve matanthauzo a Quran. Sheikh Khalid Ibrahim (Mulungu awalipire zabwino) atanthauzira ndime imeneyi momveka bwino, sadanene kuti: “Mulibe kukakamizana m’chipembedzo” ngati momwe chiarabucho chikumvekera, koma anena kuti: “Palibe kukakamiza (munthu kulowa) M'chipembedzo”.

Page 42: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

42

Mu Surah 24 (An Nur) ndime 25:

�ذ

وم ي

ف�م

و

ي

اهللا

ق دي�م

ح ال

لمون

ع

ي

أن و

اهللا

ق هو

ح ال مبني

)25( ال

“Tsiku limenelo Mulungu adzawapatsa malipiro awo a

choonadi, ndipo adzadziwa kuti Mulungu ndiye Mwini kulipira

kwachoonadi koonekera poyera.”

Ndi ndime zina zambiri. Choncho kuwawerengera anthu ntchito

zawo ndikuwapatsa malipiro awo ndiye chiweruzocho.“Maaliki

yawmiddin”: Mwini tsiku la chiweruzo.

Tsiku limeneri limatchuka ndi dzina loti: Tsiku la Qiyama,

kutanthauza kuti tsiku lodzuka mmanda ndikuyima:

ى فيه نفخ �

ر

ام � فإذا أخ

قي

ون

ظر

ن

)68( ي

“Kenako lidzaimbidwa (Lipenga)kachiwiri; pamenepo (onse)

adzauka; adzakhala akuyang'ana (modabwa: 'Nchiyani

chachitika!).” [Quran 39 (Az Zumar) kumapeto kwa ndime 68]

Lidatchulidwa kuti Tsiku la Qiyama mu Quran kokwana

makumi asanu ndi limodzi (60). Limatchedwanso kuti: Tsiku

Lomaliza ndipo lidatchulidwa kuti Tsiku Lomaliza mu Quran

kosachepera makumi awiri (20) ndi maina ena ambiri, koma

lidatchulidwa mu Quran kuti: Tsiku Lachiweruzo kokwana

khumi (10). Zikadatheka Mulungu kunena kuti: Mwini tsiku la

Qiyama, koma Mulungu mu Surah yoyambayi wagwiritsa

ntchito dzina loti: Tsiku la chiweruzo (Malipiro), chifukwa

dzinali likutenga zonse zochitika patsikuli. Kulandira malipiro

Page 43: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

43

ndiye kuti padzafunika kuti anthu awuke mmanda ndi kuyima,

kuweruzidwa kenako kupatsidwa malipiro awo, Jannah kapena

Moto. Pamene dzina loti: Tsiku la Qiyama (lowuka m’manda

ndi kuyima) likungotchula chabe zouka m’manda, silikutchula

zochitika zonse. “Tsiku lomaliza” silikutchula chochitika

chirichonse, choncho mu Surah yoyamba zidayenera kugwiritsa

ntchito dzina lomwe likukamba za zochitika zonse za tsikuli,

uko ndiye kuzama kwa mawu a Mulungu.

*******

Page 44: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

44

NDIME 5

(Ndime Yachisanu)

د إياك ب

إياك نع

و عني

)5( �ست

Iyyaka na’budu wa Iyyaka nasta’in

(5) Inu nokha tikukupembedzani, ndiponso Inu nokha

tikukupemphani chithandizo.

Quran ndi mawu a Mulungu, ndipo akulankhula apa ndi

Mulungu, akutilankhula ife okhulupilira, koma Allah

samapempha kwa aliyense:

فإن اهللا

ن غني

المني ع

ع

)97( ال

“Ndithudi, Mulungu ndiwachikwanekwane pa zolengedwa

Zake.”[Quran 3 (Aali ‘Imran) ndime 97.

Kutanthauza kuti palibe chomwe chingamuthandize

muzolengedwa Zake zonse. Mulungu akamati: “Inu nokha

tikukupemphani...”, amene akupempha si Iye, koma kuti

Mulungu akutiphunzitsa ife momwe tingayambire zinthu zathu

kuti tidziyamba ndi Bismillah, tidzimutamanda ponena kuti

Alhamdulillah ndipo akuti tidzinena kuti: “Inu nokha

tikukupembedzani ndiponso Inu nokha tikukupemphani

chithandizo.” Mu ndime zotsatirazo akupitiriza kutiphunzitsa

momwe tingamupemphere chiwongoko ndipo akuti tidziti:

“Tiongolereni kunjira yoongoka.”

Page 45: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

45

Iyyaka na’budu

“Inu nokha tikukupembedzani”

Iyyaka: “Inu nokha” Na’budu: “Timakupembedzani”, mau oti

Na’budu akuchokera ku mau oti: ‘Ibaadah

(kupembedza/kugwadira) omwe akuchokera ku mau oti: ‘Abdu

(kapolo). Timati: Abdullah (Kapolo Wa Mulungu), Abdul

Rahman, Abdul Jabbaar, Abdul Hamid ndi ena ambiri.

Kalekale, munthu akagwidwa ukapolo amakhala womvera

malamulo ndi wodzichepetsa pa maso pa bwana wake, wochita

chirichonse chomwe bwana wake walamula popanda kufunsa

chifukwa, ndipo kapolo akakanira bwana wake amapatsidwa

chilango, kumanidwa chakudya, kukwapulidwa ndi zina zotero.

Kuchita zinthu zimenezi, zomwe kapolo amachita kwa bwana

wake kumatchedwa Kupembedza. Choncho ife timatchedwa

kuti akapolo a Mulungu chifukwa cholinga chopezekera pa

dziko pano ndi kuti tidzimumvera Mulungu ndi kutsatira

malamulo Ake, kudzichepetsa pa maso pake, kuchita

chirichonse chomwe walamula, m’mene Iye akufunira popanda

kufunsa chifukwa, zimenezi zikutchedwa kuti Kupembedza

ndipo akapolo opanda kutsatira zimenezi adzapatsidwanso

chilango:

ت

اخلق

م

جن و ال

س

اإل

دون إال و

ب

ع

)56( لي

“Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti

adzindipembedza.” [Quran: 51(Adh Dhariyat) ndime 56]

Page 46: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

46

Chimenecho ndiye cholinga chomwe Mulungu adatilengera,

ndipo zinthu zina zonse zomwe timachita monga kugwira

ntchito, kudya, kugona ndizongothandizira kuti Ibaadayo ikhale

yosavuta. M’malo mwake anthu atembenuza, akupanga

kusangalala, kusonkhanitsa chuma ndi zina zotero kukhala

cholinga chenicheni ndipo Ibaadah ndiyongothandizira pa

nthawi imene moyo wathina.

Kupembedza (Ibaadah) sikupemphera Swala kokha,

Kupembedza ndi: Kudzichepetsa, Kumvera malamulo a

Mulungu ndi Kugonjera mwa Iye. Kupembedza kuli m’zinthu

zambiri, zomwe Mulungu amazikonda ndi kusangalala nazo

m’zolankhula; monga kupanga ma Dhikr (kumukumbukira

Mulungu), kupanga Dua, kulankhula zoona ndi zabwino.

Kupembedza kulinso m’zichitochito monga Kupemphera,

kupereka Zakah kapena Sadqah, kupanga Hajj, kuyendera

odwala, kukhala ndi anthu bwino ndi zina zotero.

Mu ndimeyi tikamati: “Inu nokha tikukupembedzani”

tikutanthauza kuti timachita zinthu zonsezi ndicholinga

chokusangalatsani Inu Mulungu, osati kuti anthu atione, atitame,

osatinso kuti tipeze phindu la padziko lokha. Tikaonetsetsa

tipeza kuti moyo wathu wonse wadzadza ndi Ibaadah koma

ambiri samachita ndicholinga chomusangalatsa Mulungu.

Wa iyyaka nasta’in

“Ndiponso Inu nokha tikukupemphani chithandizo.”

Tikunena kuti timapempha chithandizo kwa Mulungu Yekha,

pamenepa pakufunika timvetsetse bwino chifukwa wina akhoza

Page 47: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

47

kumafunsa kuti kodi anthu sitimathandizana? Munthu nzako

sangakuthandize? Dokotala akationaona ndikuchira

sadatithandize? Nzako akakupempha kuti umuthandize ndi 500

kwacha, pamenepo sadapemphe chithandizo?

Ndi zoona kuti anthu timathandizana, nzako akhoza

kukuthandiza, dokotala amatithandiza ndiponso nzako atha

kukupempha chithandizo. Tinene kuti tikutsutsana ndi ndime

imeneyi yoti ndi Mulungu Yekha Yemwe timamupempha

chithandizo?

Choyamba tidziwe kuti chithandizo chonse chimachokera kwa

Mulungu, ndipo Mulungu adafuna kuti chithandizo chake pa

akopolo ake chidziwapeza kudzera m’njira zosiyanasiyana,

komanso akafuna amatha kuthandiza popanda kugwiritsa ntchito

njira zimenezi. Mwachitsanzo, mukapempha Mulungu kuti

akuthandizeni ndi chakudya, Mulungu samachitsitsa kuchokera

kumwamba kufikira pa khomo panu moonekera, koma

amakusonyezani ndikukufewetserani njira yopezera

chakudyacho.

Tikapita kwa dokotala ndikuchira, timati dokotala watithandiza,

koma chithandizocho chachokera kwa Mulungu, amene

watichiritsa ndi Mulungu ndipo dokotala ndi njira imene

Mulungu adafuna kuti atithandizire. Mukalima ndikudzala

m’munda wanu, kulima ndi kudzala, mbewu ndi nthaka zonsezo

ndi njira zimene Mulungu wafuna kukuthandizirani ndi

chakudya. Ukamupempha nzako kuti akuthandize ndi 500

kwacha, nzakoyo ndi njira imene Mulungu wakufewetsera

Page 48: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

48

ndikukuthandizira. Choncho chithandizo chonse chimachokera

kwa Mulungu.

Tikamapempha chithandizo kwa munthu timayenera kudziwa

ndikukhulupilira kuti Wothandiza ndi Mulungu Yekha ndipo

munthuyo ndi njira chabe. Koma ukakhulupilira kuti iye

(munthu) ndi amene ali ndi mphamvu yokuthandiza, pamenepo

watsutsana ndi ndime imeneyi ndipo wamuphatikiza Allah ndi

zinthu zina (Shirk). Ukayika mlonda pa nyumba amene

amateteza ndi Mulungu ndipo mlondayo ndi njira imene

Mulungu akuperekera chitetezo Chake.

Ndiye tikamati “Inu nokha tikukupemphani chithandizo”

timatanthauza kuti, zonse timazisiya m’manja Mwanu chifukwa

Inu nokha ndi amene mumathandiza ndipo ife titenga njira

zomwe chithandizo chanu chimatifikira. Tilima ndi kudzala,

ndipo kudzera mu ulimiwo tithandizeni ndi chakudya. Kudzera

mwa dokotala tichiritseni ndi zina zotero.

*******

Page 49: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

49

NDIME 6

(Ndime Yachisanu ndi chimodzi)

دنا

اط اه

ر الصق�

مست

)6( ال

Ihdinas siraatal mustaqim

(6) Tiongolereni ku njira yoongoka

Tafotokoza za kupempha chithandizo m’ndime yapitayo ndipo

Mulungu m’ndime iyi akutibweretsera chinthu choyenera

kuyamba kupempha, chiongoko. Tonse timafuna kuti tidzalowe

ku Jannah, amenewo ndi mapeto a ulendo wa anthu ochita

zabwino, koma Allah mu Surah yoyambayi, pempho loyamba

kutiphunzitsa sadati: Tipatseni Jannah, koma wati: Tiongolereni

ku njira yoongoka. Chifukwa chakuti Jannah ndi mathero

pamene chiongoko ndi mayambiliro, Mulungu akatipatsa

chiongoko, zimene tizichita molingana ndi chiongokocho

zikatifikitsa ku mathero amene ali Jannah.

“Tiongolereni” mu ndimeyi ndi mawu osonyeza kupempha osati

kulamula. Bwana akanena kwa akapolo ake kuti: “Limani

munda uwu” limenelo limakhala “lamulo” kwa akapolo akewo,

pamene akapolo ake akanena kuti: “Tipatseni makasu tilime”

limenelo limakhala “pempho” kwa bwana wawoyo.

Chimodzimodzi, Mulungu akamati pangani izi, limakhala

lamulo, pamene ife akapolo Ake tikamati: “Tipangireni izi”

limakhala pempho kwa Mulungu wathu osati lamulo.

Page 50: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

50

Chiongoko (Hidaayah) chili ndi matanthauzo awiri: Pali

Chiongoko, kumusonyeza munthu njira yoyenera.

Mwachitsanzo munthu wafika pa msewu womwe wagawikana

pawiri, sakudziwa kuti ndi nsewu uti umene ukamufikitse

kumene akupita, adzayenera kupeza munthu amene akudziwa,

amuuze kuti komwe akupitako atenge nsewu uwu ndipo

akatenga winawu asochera. Munthu ameneyu wamuongolera

pomusonyeza njira yoyenera ndi kumuchenjeza za njira inayo.

Imeneyo ndiye ntchito ya Atumiki komanso anthu amene atenga

mipando ya Atumiki (ma Sheikh), kuongolera anthu powauza

njira ya ku Jannah ndikuwachenjeza za njira yaku Moto.

Ndiye pali Chiongoko (Hidaayah) chomwe ndikuika madalitso

ndi Imaan mu mtima wa munthu kuti atsate ndikugwiritsa

ntchito njira yoongoka, m’kulankhula kwina tingati, kutsekula

mtima wa munthu kuti akhale okhulupilira ndi wochita zabwino.

Amene amatsekula mtima wa munthu kuti Imaan imeneyi ilowe

ndi Mulungu Yekha. Ndichifukwa chake timapeza ndime ziwiri

kapena zingapo zagwiritsa ntchito mau amenewa oti: Chiongoko

(Hidaayah) mosiyana ndipo zimamveka ngati ndimezi

zikutsutsana. Anthu odana ndi chisilamu amatenga ndime

zimenezi ndikupezerapo mwayi wonena kuti Quran imadzitsutsa

yokha. Vuto ndi kusazindikira, ndimezi nazi:

Surah 42 (Ash Shura) kumapeto kwa ndime 52:

إنك

دي و اط إ� ل�

ق� صرست

)52( م

“Ndithu iwe (Muhammad) ukuongolera kunjira yoongoka,”

Page 51: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

51

Mu ndimeyi Mulungu akumuuza Mtumiki (SAW) momveka

bwino kuti iye Mtumiki (SAW) akuwaongolera anthu ku njira

yoongoka. Pamene mu Surah 28 (Al Qasas) ndime 56, Mulungu

akuti:

دي ال إنك ن �

م

بتل�ن أحب

و

دي اهللا

ن �

م �شاء

لم

أع

هو

و

دين

ت

مه

)56( بال

“Ndithu, iwe sungathe kumuongola amene ukumfuna, koma

Mulungu amamuongola amene wamfuna. Ndipo Iye akudziwa za

amene ali oongoka.”

Kuchichewa tikutha kumva kusiyana kwa ndime zimenezi,

yoyambayo akuti “Kuongolera” yachiwiriyo akuti “Kuongola.”

Pamene kuchirabu agwiritsidwa ntchito mau amodzi. Choncho

ndimezi sizikutsutsana, mu ndime yoyambayo Mulungu

akumuuza Mtumiki (SAW) kuti iye akuwalozera anthu njira

yoyenera kutsata, njira yoongoka, pamene ndime yachiwiriyo

Mulungu akumuuza Mtumiki (SAW) kuti iye sangathe

kutsekula mtima wa munthu ndikumuyika Imaan ndi

chikhulupiliro kuti atsate njira yoongoka, zimenezo amachita

ndi Mulungu.

Quran ndi mawu a Mulungu ndipo sizingatheke kupezeka

kutsutsana, ngati mungapeze kutsutsana ndiye kuti penapake

simunapamvetse bwino choncho osafulumira kunena kuti Quran

ikudzitsutsa yokha, m’malo mwake afunseni amene

akuzindikira kuti akufotokozereni bwino.

Page 52: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

52

Siraat (Njira)

Mu ndimeyi, Siraata ndi mawu amene atanthauzidwa kuti Njira

m'chichewa. Njira, ndi m'sewu kapena ndondomeko imene

munthu amatsata kuti athe kukwaniritsa kapena kukafika

kumene iye akupita. Zimakhala zovuta kuti munthu akafike

kumene iye akupita ngati sakutsatira njira yoyenera. Choncho,

mawu omaliza a ndime ino akufotokoza chizindikiro cha njira

yoyenera..

Mustaqeem (yowongoka)

Njira yowongoka ndi imene ili yosakhotakhota, ndipo ndi njira

imene imakhala yofupika kuposa njira yokhotakhota.

*******

Page 53: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

53

NDIME 7

(Ndime Yachisanu ndi chiwiri)

اط

صرين ا�

ت

م

ع

م أن ل�

ع

ضوب غري

غ

مم ال ل�

ال ع

الني و )7( الض

Siraatalladhina an’amta ‘alayhim, ghayril magh-dhubi

‘alayhim waladh dhaallin

(7) Njirayaomwe mudawapatsa chisomo; osati ya amene

adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera.

Ndime imeneyi ikupitiriza kufotokoza za njira yoongoka imene

yatchulidwa m’ndime yomwe yangothayo: “Tiongolereni ku

njira yoongoka.”

Akamati njira yoongoka m’ndimeyi akutanthauza chani?

Siraatalladhina an’amta ‘alayhim

“Njira ya omwe mudawapatsa chisomo…”

Ndime imeneyi ikutiwuza kuti njira yoongokayi ndi yomwe

adatsata anthu omwe adapatsidwa chisomo ndi Mulungu. Kodi

omwe adapatsidwa chisomo ndi ndani, tiwadziwe kutinso

tidziwe njira imene iwo adatsata? Tikawerenga Quran tikupeza

Surah 4 (An Nisaa) ndime 69 yawatchula omwe adapatsidwa

chisomo:

ن

م

طع و ي

ول اهللا

س

الر

فأول�ك و

ع

مين ا�

م

ع

أن

اهللا

م ع ل�ني من يقني النبي د الص

و

هداء الش

الحني و الص

ون

س

ح

فيقا أول�ك و

)69( ر

Page 54: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

54

“Ndipo amene angamvere Mulungu ndi Mtumiki Wake, iwowo

ndi omwe adzakhale pamodzi ndi omwe Mulungu adawapatsa

chisomo (adawadalitsa), kuyambira Aneneri, Olungama, ma

Shahidi (asilamu ofela kunkhondo) ndi anthu abwino. Taonani

ubwino wokhala nawo pamodzi iwowo!”

Ndimeyi yanena kuti amene adapatsidwa chisomo ndi

kuyambira: Aneneri, Olungama, ma Shahid ndi anthu abwino

(ochita zabwino). Chisomo (Ni’mah) chimatchedwanso kuti

mtendere, ndi chirichonse chabwino pa moyo wa munthu, kuona

ndi chisomo, kuyenda, kupuma, kukhala msilamu ndi chisomo,

kuti tiyambe kuwerenga chisomo sitingakwanitse. Mulungu mu

Surah 16 (An Nahl) ndime 18 akuti:

إن

وا و ة تعد

م

نع وها ال اهللا

ص

إن تح ح� اهللا

)18( لغفورر

“Ngati mutayesera kuwerengera mtendere wa Mulungu

simungathe kuuwerengera (wonse); ndithudi, Mulungu

ndiwokhululuka kwambiri, ndiwachisoni.”

Mtendere umenewu tikuona kuti amapatsidwa anthu onse

okhulupilira ndi osakhulupilira omwe, tsopano ndimeyi ikuti

amene adapatsidwa chisomochi ndi Aneneri, Olungama ma

Shahid ndi ochita zabwino. Zikuonetsa kuti chisomo

chimenechi ndi cha mtundu wina osati chisomo chomwe

amapatsidwa anthu onse, monga maso, makutu ndi zina zotero.

Choncho ma sheikh ena amanena kuti chisomo chimenechi ndi:

Kusonyezedwa njira ya choona, ndikupatsidwa mtima wotha

kuyigwiritsa njira imeneyi (Imaan\Chikhulupiliro).

Page 55: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

55

Amenewa ndi amene amatsata njira yoongoka choncho tikafuna

kudziwa kuti njira yoongoka ndi chani, tiwafunse amene

atchulidwa apawa. Mu Quran m’neneri amene wafotokoza kuti

njira yoongoka ndi chani, ndi M’neneri Yesu (AS). Surah 3

(Aali ‘Imran) ndime 51, Surah 19 (Maryam) ndime 36 komanso

Surah 43 (Az Zukhruf) ndime 64.

Surah 19 (Maryam) ndime 36:

إن

و � اهللا

ب�م ر

ر

و

دوه

ب

هذا فاع

اط

ق� صر

ست

)36( م

“(Yesu adati:) "Ndipo ndithu, Mulungu ndi Mbuye wanga

ndiponso Mbuye wanu.Choncho m’pembedzeni; iyi njira

yolunjika (yokufikitsani ku mtendere.)”

Yesu (AS) akuwauza anthu kuti kukhulupilira kuti Mbuye ndi

Mulungu, ine (Yesu) simbuye, Mbuye wanga ndi Mbuye wanu

ndi Mulungu, ndi kuti omupembedza ndi Mulungu osati ine

(Yesu), musapemphere mu dzina la ine ndipo pempherani

m’dzina la Mulungu, imeneyi ndiye njira yoongoka. Mu ndime

zitatu zomwe zafotokoza kuti njira yoongoka ndi chani,

amalankhula ndi Yesu (AS). Ndipo Mulungu akuikira kumbuyo

mawu a Yesu oti kupembedza Mulungu Yekha ndiye njira

yoongoka mu Surah 36 (Yasin) ndime 60 ndi 61, Mulungu

akuti:

م أل

هد

ني إلي�م أعاب

ي

م

آد

دوا ال أن

ب

تع

يطان الش ل�م إنه

دو

ع

بني

)60( م

أن

دو� وب

هذا اع

اط

ق� صر

ست

)61( م

Page 56: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

56

“(60) Kodi sindidakulangizeni, E!inuana a Adamu kuti

musapembedze Satana; ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa

inu. (61) Ndikuti ndipembedzeni Ine; imeneyi ndi njira yolunjika

(yoongoka).”

Zili ngati kuti Yesu (AS) adadziwa kuti akadzachoka anthu

adzamutcha mwana wa Mulungu ndikumupembedza.

Pachifukwa chimenechi tikupeza kuti Yesu (AS) adalankhula ali

wakhanda ndipo mau oyamba kuwauza anthu adali oti: “Ine

ndine kapolo wa Mulungu”:

بد إ� قال

ع اهللا آتا�

اب

�ت

لني ال

ع

ج

)30( نبيا و

“(Mwanayo) adanena: "Ine ndine kapolo wa

Mulungu.Wandipatsa Buku ndikundichita kukhala

Mneneri.”Surah 19 (Maryam) ndime 30.

Zikadatheka kungonena kuti “ine ndine Mtumiki wa Mulungu

ndi Mneneri Wake” koma Yesu (AS) adayamba ndikuti ine

ndine kapolo wa Mulungu, chifukwa mawu amenewa

tikawamvetsetsa bwino tipeza kuti akutsutsa zoti Yesu (AS) ndi

mwana wa Mulungu. Palibe amene angamupange mwana wake

kukhala m’gulu la akapolo ake omugwilira ntchito, choncho

ngati Yesu (AS) akuti ine ndine kapolo wa Mulungu sizotheka

kuti akhale mwana wa Mulungu. Akadangonena kuti ine ndine

Mtumiki ndi Mneneri wa Mulungu, zikadanenedwa kuti

ndizotheka mwana wako kukhala wotumikira.

Page 57: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

57

Choncho mu ndimeyi tikamati “Tiongolereni ku njira yoongoka.

Njira ya omwe adapatsidwa chisomo…” njira yake ndi:

“Kupembedza Mulungu yekha.”

Ghayril magh-dhubi ‘alayhim

“…Osati ya amene adakwiyiridwa (ndi Inu)

Ndime 7 ikupitiriza kunena kuti njira yake osati ya omwe

adakwiyiridwa ndi Mulungu osatinso njira ya omwe adasochera.

Mabuku a Tafsir amatiuza kuti amene adakwiyiridwa ndi

Ayuda, kutengera ndime 60 mu Surah 5 (Al Maidah) yomwe

ikukamba za Ayuda motere:

قل

أنبئ�م هل ة ذلك من ��

ثوب

د م

عن ن اهللا

م نه

لع

اهللا

غضب

ليه و

ل ع

ع

ج

و

م

م�

ة د

قر

ال

خنازير

ال

د و

ب

ع

أول�ك الطاغوت و

كانا شر

أضل م

ن و

اء ع

و

بيل س )60( الس

Nena: "Kodi ndikuuzeni za uja amene ali ndimalipiro oipa kwa

Mulungu kuposa izi? Ndiomwe Mulungu wawatemberera ndi

kuwakwiira ndi kuwasandutsa ena kukhala anyani ndi nkhumba,

ndi opembeza Satana. Awo ndiwo okhala ndi malo oipa,

ndiponso osokera njira yowongoka."

Mulungu adawatembelera, kuwakwiyira ndi kuwasandutsa ena

mwa iwo anyani ndi nkhumba. Amene adasandutsidwa ena mwa

iwo kukhala anyani ndi Ayuda, umo ndi m’mene ma Sheikh

ambiri amatiuzira. Tikufunika kumvetsetsa, sizikutanthauza kuti

Ayuda okha ndi amene adakwiyiridwa ndi Mulungu, komanso

Mulungu sadawakwiyire iwo pokhala kuti ndi Ayuda koma

Page 58: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

58

chifukwa cha kukanira kwawo chilungamo akuchidziwa

komanso kupha Aneneri. Surah 2 (Al Baqarah) ndime 61,

kumapeto kwa ndime imeneyi Mulungu akuti:

تضرب

و

م ل�

ع � ا� سكنة

مال

وا و

اء

ب

بغضب و

من م ذلك اهللا

كانوا بأ�

ون

فر

ك ي

ات بآي اهللا

تلون

ق

ي

ني و النبي

ق بغري

ح

ا ذلك ال

وا بم

ص

كانوا ع

و

دون

ت

ع

)61( ي

“…Potero adapatsidwa kunyozeka ndi kusauka; nabwelera ndi

mkwiyo wa Mulungu. Zimenezo n'chifukwa chakuti iwo sadali

okhulupilira zisonyezo za Mulungu, ndikuti adali kupha

Aneneri a Mulungu popanda chifukwa. Zidali tero chifukwa cha

kunyoza kwawo, ndipo adali olumpha malire.”

Choncho okwiyiridwa ndi Mulungu si Ayuda okha, koma

aliyense amene amachita zimene Ayuda adachita, kukanira

chilungamo akuchidziwa, kupha Aneneri ndi kudumpha malire

m’kukanira kwawo.

Waladh-dhaallin

“Osatinso ya omwe adasokera.”

Mulungu mu ndimeyi akupitiriza kuti osatinso njira ya omwe

adasokera. Amene adasokera ndi Akhristu, kutengera Hadith:

“Ibn Hatim adati: Ndidamufunsa Mtumiki (SAW) za mau a

Mulungu oti: {Osati (njira) ya omwe adakwiyiridwa} iye

(Mtumiki) adati: Anthu ake ndi Ayuda, {Osatinso ya omwe

adasokera} iye adati: Akhristu.”

Page 59: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

59

Kusochera ndikutenga njira yolakwika ndikumaganiza kuti

ikakufikitsa kumene ukufuna. Kusiyana kwa Ayuda ndi Akristu

ndikwakuti, Ayuda, amaidziwa njira yoongoka ndi yachoonadi,

koma amayibisa ndikumatsatira zawozawo. Pamene Akristu

samayidziwa njira yoongoka, safunanso kufufuza kuti athe

kuyipeza, mmalo mwake amatsatira njira yomwe iwo akuganiza

kuti ndiyoona ndikuti ikawafikitsa ku ufumu wa kumwamba,

umo ndi momwe adasochelera. Omwe adasokera si Akhristu

okha, koma aliyense amene samadziwa choona ndipo safuna

kuchidziwa koma kutsata njira yolakwika kumaganiza kuti

ndiye yoongoka, ndipo Akhristu ndi amene ali owoonekera.

*******

__________________

AMEEN

نيآم

Ameen

Ndi Sunnah kwa amene wawerenga kapena kumvera Surat Al

Fatihah kunena kuti: Ameen.

Mawu oti: “Ameen” amatanthauza kuti: “Ambuye pangani”

kutanthauza kuti Ambuye Mulungu tipangireni zimene

takupemphanizi. Amatanthauzanso kuti: Ambuye yankhani

(pempho langa\lathu), tanthauzo lachiwirili ndi limene ma

Sheikh ambiri amasankha.

Page 60: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

60

Ndime ziwiri zomaliza mu Surat Al Fatihah ndi “Dua”

(pempho): “Tiongolereni ku njira yoongoka. Njira ya omwe

mudawapatsa chisomo; osati ya amene adakwiyiridwa (ndi

Inu) osatinso ya omwe adasokera.” Ameen (Ambuye

tiyankheni pempho lathuli.)

Mau oti Ameen siochokera mu Quran, ndi mau a Jibril,

ndichifukwa chake samalembedwa limodzi ndi Surayi ngati

momwe “Bismillah” amalembedwera.

Pali ma Hadith ambiri omwe amatilimbikitsa kunena Ameen

tikawerenga Surat Al Fatihah ena mwa iwo ndi awa:

Abu Hurairah adati: Mtumiki (SAW) amati akawerenga:

{Ghayril magh-dhubi ‘alayhim wala-dhaallin} amanena kuti:

“Ameen.”-Abu Daud-

Hadith ina ya Abu Hurairah, Mtumiki (SAW) adati: “Imaam

akanena kuti Ameen inunso mudzinena Ameen chifukwa

ndithudi, amene Ameen wake afanane\atsatane ndi Ameen wa

Angelo, Mulungu amamukhululukira machimo ake onse

am’mbuyo.” -Bukhari, Muslim-

_________________________

Page 61: Ndime7 (Surat Al Fatehah)

61

MABUKU OMWE AMAONEDWA KWAMBIRI

POLEMBA BUKU LIMENERI:

1. Quran Ya Chichewa (Sheikh Khalid Ibrahim).

2. Tafsir Al Sha’rawiy (Sheikh Muhammad Mutawally Al-

Sha’rawiy).

3. Tafsir Al Wasit (Sheikh Muhammad Sayyid Tantawiy –

Sheikhul Azhar).

4. Tafsir Ibn Kathir.

5. Tafsir Ibn Abbas.

6. Tafsir Ayaatil Ahkaam.

7. Fi Rihaabit Tafsir (Sheikh Abdul Hamid Kishk).

Kuphatikizapo ma buku ena omwe amaonedwa mwapatalipatali.