32
34567 APRIL 2016 Zilembo Zazikulu GAWO 1 May 30–June 5 Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika TSAMBA 3 June 6-12 “Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake” TSAMBA 17

wlp16.04-CN-1 - download-a.akamaihd.net · The Watchtower (ISSN 0043-1087) Issue 6 April 2016 is published monthly with an additional issue published in January, March, May, July,

Embed Size (px)

Citation preview

34567APRIL 2016

Zilembo Zazikulu GAWO 1

May 30–June 5Yehova AmadalitsaAnthu Okhulupirika

TSAMBA 3

June 6-12“Mulole Kuti

Kupirira KumalizeKugwira Ntchito Yake”

TSAMBA 17

The Watchtower (ISSN 0043-1087) Issue 6 April 2016 is published monthly with an additionalissue published in January, March, May, July, September, and November by Watchtower Bibleand Tract Society of New York, Inc.; L. Weaver, Jr., President; G. F. Simonis, Secretary-Treasurer; 1000 Red Mills Road,Wallkill, NY 12589-3299, and printed by WatchTower Bible andTract Society of South Africa NPC, 1 Robert Broom Drive East, Rangeview, Krugersdorp, 1739.� 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Printed in South Africa.

34567APRIL 2016

Vol. 137, No. 6 CHICHEWA

NKHANI ZOPHUNZIRA

˝ Yehova Amadalitsa Anthu OkhulupirikaNkhaniyi ikufotokoza zimene Yefita ndi mwana wakewamkazi anachita kuti apitirize kutsatira mfundo za Ye-hova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Tiphunzi-ranso kuti kukhala okhulupirika kwa Mulungu n’kofu-nika kwambiri kuposa chilichonse.

˝ “Mulole Kuti Kupirira Kumalize KugwiraNtchito Yake”

Tiyenera kupirira mpaka mapeto kuti tidzalandire moyowosatha. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu 4 zimene zingati-thandize kupirira komanso zitsanzo za anthu atatu ame-ne anakhalabe okhulupirika pamene ankakumana ndimavuto. Ikufotokozanso mmene kupirira kungamalizirentchito yake kwaMkhristu aliyense.

Magaziniyi sitigulitsa.Timaipereka ngati njiraimodzi yophunzitsira anthuBaibulo padziko lonsendipo ndalamazoyendetsera ntchitoyi ndizimene anthu amaperekamwa kufuna kwawo.Ngati mukufuna kuperekapitani pawebusaiti yathuya www.jw.org/ny.

Malemba onsem’magaziniyi akuchokeramu Baibulo la DzikoLatsopano la MalembaOpatulika, lolembedwam’Chichewa chamakono,kupatulapo ngatitasonyeza Baibulo lina.

APRIL 2016 GAWO 1 3

PA NTHAWI ina Yefita atapita kunkhondomwana wake wamkazi ankangoyembekezera kutibambo akewo abwerako liti. Kenako mwanayoanawaona akubwera ndipo anasangalala kwa-mbiri chifukwa iwo anapambana pa nkhondoyo.1, 2. Kodi n’chiyani chinachitikira Yefita ndi mwanawake?

Yehova AmadalitsaAnthu Okhulupirika

“Mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupirirondi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu

analonjeza monga cholowa chawo.”—AHEB. 6:12.

NYIMBO: 86, 54KODI MUNGAYANKHE BWANJI?Kodi chitsanzo cha Yefita ndi mwana wakechingatithandize bwanji kupewa kutengera anthu am’dzikoli?Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimenezingakuthandizeni mukasemphana maganizo ndi ena?Kodi mfundo za m’nkhaniyi zingakuthandizeni bwanjikukhala ndi mtima wodzipereka?

4 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

Nthawi yomweyo ananyamuka kukawachingami-ra akuvina. Koma bambo akewo atamuona ana-yamba kung’amba zovala zawo n’kunena kuti:“Kalanga ine mwana wanga! Wandiweramitsandi chisoni.” Kenako Yefita ananena mawu oso-nyeza kuti tsogolo la mwana wakeyo lisinthiratu.Koma mwanayo anasonyeza kuti anali ndi chi-khulupiriro cholimba chifukwa anauza bamboakewo kuti atsatire zimene analonjeza Mulungu.Iye ankakhulupirira kuti zonse zimene Yehovaanganene ndi zoyenera kwa iyeyo. (Ower. 11:34-37) Zimene anachitazi zinasangalatsa kwambiriYefita chifukwa anadziwa kuti Yehova awadali-tsa.

2 Yefita komanso mwana wake ankakhulupi-rira kwambiri Yehova ngakhale pa nthawi yovu-ta. Iwo ankaona kuti chofunika kwambiri ndikusangalatsa Mulungu.

APRIL 2016 GAWO 1 5

3 Kukhala ndi chikhulupiriro cholimba si ko-phweka. Pamafunika “kumenya mwamphamvunkhondo yachikhulupiriro.” (Yuda 3) Yefita ndimwana wake anakhalabe okhulupirika kwa Yeho-va. Tiyeni tikambirane mavuto amene iwo anaku-mana nawo. Izi zitithandiza kuti nafenso tikhalendi chikhulupiriro cholimba.

ANAKHALABE OKHULUPIRIKAM’DZIKO LOIPA

4 Yefita ndi mwana wake ankaona mavutoamene anabwera chifukwa choti Aisiraeli anasiyaYehova. M’mbuyomo, Aisiraeli anauzidwa kutiawononge anthu onse osalambira Yehova ameneankakhala m’Dziko Lolonjezedwa. (Deut. 7:1-4)3. Kodi zimene Yefita ndi mwana wake anachita zingati-thandize bwanji?4, 5. (a) Kodi Yehova anapereka lamulo liti kwa Aisirae-li pamene ankalowa m’Dziko Lolonjezedwa? (b) Malingandi Salimo 106, kodi kusamvera kwa Aisiraeli kunabwere-tsa mavuto otani?

Koma iwo sanachite zimenezi ndipo anayambakulambira mafano komanso kutengera makhali-dwe oipa a Akanani.—Werengani Salimo 106:34-39.

5 Izi zinakwiyitsa kwambiri Yehova ndipo ana-siya kuwateteza. (Ower. 2:1-3, 11-15; Sal. 106:40-43) Pa nthawiyi, zinali zovuta kuti mabanja oopaMulungu akhalebe okhulupirika. Koma Baibulolimasonyeza kuti panali anthu ena okhulupirikaamene ankasangalatsa Mulungu. Anthu ake ndimonga Elikana, Hana, Samueli ndiponso Yefitandi mwana wake.—1 Sam. 1:20-28; 2:26.

6 Anthu ambiri m’dzikoli amachita zinthungati Akanani akale ndipo amakonda chiwerewe-re komanso chuma. Koma mofanana ndi Aisira-eli, Yehova watipatsa malangizo oti azititeteza.Choncho tiyenera kupewa zinthu zolakwika zime-6. Kodi masiku ano anthu amakonda chiyani, nanga ifeyotiyenera kuchita chiyani?6 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

ne Aisiraeli ankachita. (1 Akor. 10:6-11) Koma-nso tiyenera kusamala kuti tisayambe kuchita zi-nthu ngati Akanani. (Aroma 12:2) Kodi inuyomukuyesetsa kuchita zimenezi?

ANAKHALABE WOKHULUPIRIKAATAKUMANA NDI MAVUTO

7 M’masiku a Yefita, kusamvera kwa Aisiraelikunachititsa kuti akhale akapolo a Afilisiti koma-nso Aamoni. (Ower. 10:7, 8) Kuwonjezera pa-menepa, Yefita ankavutitsidwa ndi anthu ameneankatsogolera Aisiraeli komanso abale ake. Mwa-chitsanzo, abale ake ena anamuthamangitsa chi-fukwa choti anali mwana wa mayi wina. Anatisankayenera kulandira cholowa ngati mwana wo-yamba kubadwa. (Ower. 11:1-3) Yefita sanalolekuti zochita za abale akewa zimusokoneze. Ti-kutero chifukwa atapemphedwa kuti akathandize7. (a) Kodi anthu anamuchitira zotani Yefita? (b) KodiYefita anatani?APRIL 2016 GAWO 1 7

abale akewo, anapita mosanyinyirika. (Ower. 11:4-11) Kodi n’chiyani chinathandiza Yefita kutiachite zonsezi bwinobwino?

8 N’zoona kuti Yefita anali msilikali wampha-mvu, koma ankaphunziranso zimene Mulunguanachitira anthu ake. Iye ankadziwa bwino mbiriya Aisiraeli ndipo ankazindikira zinthu zoyenerandi zosayenera pamaso pa Yehova. (Ower. 11:12-27) Yefita akamasankha zochita ankatsatiramfundo za m’Chilamulo. Ankadziwa kuti Yehovaamafuna kuti anthu ake azikondana osati ku-sungirana zifukwa. Chilamulo chinkanena kutimunthu ayenera kuthandiza anzake ngakhalensoanthu amene amadana naye.—Werengani Ekiso-do 23:5; Levitiko 19:17, 18.

9 Yefita ayenera kuti ankaganizira chitsanzocha anthu ngati Yosefe. Paja Yosefe anathandiza8, 9. (a) Kodi ndi mfundo ziti za m’Chilamulo zimene zi-namuthandiza Yefita? (b) Kodi Yefita ankaona kuti chofu-nika kwambiri n’chiyani?8 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

abale ake ngakhale kuti ‘ankadana naye.’ (Gen.37:4; 45:4, 5) Kuganizira zimenezi kunathandizaYefita kuti achite zinthu zosangalatsa Yehova. Zi-mene abale ake anamuchitira ziyenera kuti zina-muwawa kwambiri, komabe sizinamulepheretsekutumikira Yehova komanso anthu ake. (Ower.11:9) Iye ankaona kuti kumenya nkhondo poye-retsa dzina la Yehova n’kofunika kwambiri kusi-yana ndi kulimbana ndi abale akewo. Ankafuni-tsitsa kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndipozotsatira zake zinali zabwino kwa iyeyo komansokwa anthu ena.—Aheb. 11:32, 33.

10 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yefi-ta anachita? Mwina pali Mkhristu wina ame-ne anakulakwirani kapena kukukhumudwitsani.Ngati ndi choncho, musalole kuti nkhani ime-neyo ikulepheretseni kusonkhana kapena kutu-mikira Yehova limodzi ndi mpingo. Potengera10. Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji pa-mene ena atilakwira?APRIL 2016 GAWO 1 9

chitsanzo cha Yefita, tizitsatira mfundo za Yeho-va n’kumachitabe zabwino ngakhale titakumanandi mavuto.—Aroma 12:20, 21; Akol. 3:13.

MUNTHU WODZIPEREKA AMASONYEZAKUTI ALI NDI CHIKHULUPIRIRO

11 Yefita ankadziwa kuti akufunika thandizola Yehova kuti apulumutse Aisiraeli m’manjamwa Aamoni. Iye analonjeza Yehova kuti: ‘Ndi-dzapereka aliyense amene adzatuluke m’nyumbayanga kudzandichingamira pamene ndikubweramwamtendere kuchokera kwa ana a Amoni. Ndi-dzam’pereka monga nsembe yopsereza.’ (Ower.11:30, 31) Kodi pamenepa ankatanthauza chi-yani?

12 Yehova amadana ndi kupha anthu n’choli-nga choti aperekedwe nsembe. Choncho Yefita sa-nkafuna kupha aliyense n’kumupereka nsembe.11, 12. Kodi Yefita analonjeza chiyani kwa Yehova, nangazimene analonjezazo zinkatanthauza chiyani?10 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

(Deut. 18:9, 10) Aisiraeli analamulidwa kuti azi-pereka nyama yathunthu ngati nsembe yopsereza.Choncho Yefita ankatanthauza kuti munthu ame-ne adzamuchingamireyo adzatumikira pachihemacha Yehova kwa moyo wake wonse. Yehova ana-mva pemphero la Yefita ndipo anamuthandizakugonjetsa adani ake onse. (Ower. 11:32, 33)Koma kodi Yefita akanapereka ndani kuti akhalengati “nsembe yopsereza”?

13 M’ndime yoyamba ija tanena kuti pameneYefita ankabwera, mwana wake wamkazi ndi ame-ne anamuchingamira. Apa tsopano zinthu zina-vuta chifukwa mwana wake anali yekhayo. Ndiyekodi Yefita anatani? Kodi anaperekadi mwanawakeyu kuti akatumikire pachihema moyo wakewonse?

14 Apanso Yefita anagwiritsa ntchito mfundo13, 14. Kodi mawu a pa Oweruza 11:35 akusonyeza bwa-nji kuti Yefita anali ndi chikhulupiriro cholimba?APRIL 2016 GAWO 1 11

za m’Baibulo kuti adziwe zoyenera kuchita.Mwina anakumbukira lemba la Ekisodo 23:19.Lembali limati tiyenera kupereka kwa Yehovazinthu zabwino koposa. Komanso Chilamulo chi-nkati: “Munthu akalonjeza kwa Yehova, . . .asalephere kukwaniritsa mawu ake. Achite ma-linga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake.”(Num. 30:2) Mofanana ndi Hana amene anakha-laponso m’nthawi yake, Yefita ankafunika kuchi-ta zimene analonjeza ngakhale kuti zinali zovu-ta kwa iye komanso mwana wakeyo. Paja Yefitaanalibe mwana wina. Choncho ankayembekezerakuti mwana wakeyu ndi amene adzatenge dzi-na lake komanso kulandira cholowa cha banjalawo. (Ower. 11:34) Ngakhale zinali choncho, Ye-fita ananena kuti: “Ndatsegula pakamwa pangapamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubwezamawu anga.” (Ower. 11:35) Yehova anasangalalakwambiri ndi zimene Yefita anachita ndipo ana-12 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

mudalitsa. Kodi nanunso mungathe kuchita zi-mene Yefita anachitazi?

15 Pamene tinkadzipereka kwa Yehova tina-mulonjeza kuti tizichita zonse zimene akufuna.Tinkadziwa kuti tiyenera kudzimana zinthu zinakuti tikwanitse kuchita zimenezi. Ngakhale zilichoncho, nthawi zina zimakhala zovuta ngati ta-pemphedwa kuchita zinthu zimene sitinkaganizakuti tingachite. Komabe tikamalolera timasonye-za kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Ndipotuzotsatira zake zimakhala zabwino chifukwa Yeho-va amatidalitsa kwambiri. (Mal. 3:10) Tsopanotiyeni tikambirane chitsanzo cha mwana wa Ye-fita.

16 Lonjezo la Yefita linali losiyana ndi la15. Kodi ambirife tinalonjeza chiyani kwa Mulungu, na-nga tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika?16. Kodi mwana wa Yefita anatani atadziwa kuti bamboake analonjeza kuti iyeyo azikatumikira pachihema? (Ona-ni chithunzi patsamba 5 m’magazini ya zithunzi.)APRIL 2016 GAWO 1 13

Hana. Hana anapereka Samueli kuti azikatumi-kira pachihema monga Mnaziri. (1 Sam. 1:11)Anaziri ankatha kukwatira komanso kukhala ndiana. Koma mwana wa Yefita sakanakwatiwa ka-pena kukhala ndi ana chifukwa anali ngati “nse-mbe yopsereza.” (Ower. 11:37-40) Sizinali zo-phweka kuti mwana wa Yefita alolere zimenebambo ake analonjeza kwa Mulungu. Popeza ba-mbo ake anali mtsogoleri wa Isiraeli komansowodziwa kumenya nkhondo, mtsikanayu akana-tha kukwatiwa ndi mwamuna wabwino kwambi-ri. Koma m’malomwake, anayenera kukhala wa-ntchito wamba n’kumatumikira pachihema. Kodimwana wa Yefitayu anatani? Iye anasonyeza kutiankaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika ndi-po anati: “Bambo, ngati mwatsegula pakamwapanu pamaso pa Yehova, ndichitireni mogwiriza-na ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” (Ower.11:36) Mtsikanayu analolera kuti asakwatiwe14 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

ndiponso kuti asakhale ndi ana n’cholinga chotiazitumikira Yehova. Kodi ifeyo tingamutsanzirebwanji?

17 Masiku anonso, abale ndi alongo achinya-mata amalolera kuti asalowe m’banja kapena asa-khale ndi ana kuti azichita zambiri potumikiraYehova. Palinso achikulire ena amene amadzipe-reka kwambiri. Amalolera kusiya ana ndi zidzu-kulu kuti agwire ntchito zomangamanga, aloweSukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu kapenaakalalikire kudera lina. Pa nthawi yoitanira anthuku Chikumbutso abale ndi alongo enanso amaye-setsa kuti akhale ndi nthawi yambiri yogawiranawo timapepala. Yehova amasangalala akamao-na zonsezi ndipo sadzaiwala ntchito yawo ko-manso chikondi chimene amachisonyeza. (Were-ngani Aheberi 6:10-12.) Kodi nanunso mukhoza17. (a) Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Yefi-ta ndi mwana wake? (b) Kodi lemba la Aheberi 6:10-12, li-kutilimbikitsa bwanji kukhala odzipereka?APRIL 2016 GAWO 1 15

16 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

kuwonjezera zimene mumachita potumikira Ye-hova?

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO18 Yefita anakumana ndi mavuto ambiri pa

moyo wake koma ankasankha zinthu mogwiriza-na ndi maganizo a Yehova. Iye sankatengera zo-chita za anthu ena ndipo anakhalabe wokhulupiri-ka ngakhale kuti anthu ena ankamuchitira zoipa.Popeza Yefita ndi mwana wake anadzipereka kwa-mbiri potumikira Yehova, anadalitsidwa kwambi-ri. Iwo ankatsatira mfundo za Yehova pa nthawiimene anthu ambiri ankazinyalanyaza.

19 Baibulo limatilimbikitsa kuti tizitsanzira“anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kulezamtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analo-njeza.” (Aheb. 6:12) Tiyeni tiziyesetsa kutsanziraYefita ndi mwana wake. Tikatero tidzaona umbo-ni wakuti Yehova amadalitsa anthu okhulupirika.18, 19. Kodi Yefita ndi mwana wake anachita chiyani, na-nga tingawatsanzire bwanji?

APRIL 2016 GAWO 1 17

NKHONDO ya pakati pa Aisiraeli ndi Amidiya-ni inali itafika poipa kwambiri. Asilikali achiisiraeliomwe ankatsogoleredwa ndi Gidiyoni anathamangi-tsa adani awowo usiku wonse kwa mtunda wama-kilomita pafupifupi 32. Baibulo limati: “Kenako,1, 2. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Gidiyoni ndiasilikali ake 300 anachita? (Onani chithunzi pamwambapam’magazini ya zithunzi.) (b) Mogwirizana ndi lemba la Luka21:19, n’chifukwa chiyani tiyenera kupirira?

Mulole KutiKupirira Kumalize

Kugwira Ntchito Yake”“Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake,kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali

zonse, osaperewera kalikonse.”—YAK. 1:4.

NYIMBO: 135, 139KODI TINGAYANKHE BWANJI?Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira?Tchulani zitsanzo za anthu ena amene anapirira.Kodi munthu angatani kuti “kupirira kumalize kugwirantchito yake”?

18 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

Gidiyoni anafika ku Yorodano n’kuwoloka mtsinje-wo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nawo aja,ali otopa.” Komabe Gidiyoni ndi asilikali akewo ana-li asanapambane nkhondoyo chifukwa adani okwa-na 15,000 anali adakalipo. Aisiraeli anali ataponde-rezedwa ndi a Midiyani kwa zaka zambiri ndipoankadziwa kuti iyi sinali nthawi yoti asiye kume-nya nkhondo. Choncho, anapitirizabe ‘kuthamangi-tsa’ a Midiyani mpaka kuwagonjetsa.—Ower. 7:22;8:4, 10, 28.

2 Masiku ano nafenso tikumenya nkhondo yovu-ta kwambiri. Tikulimbana ndi Satana, dziko loipalikomanso matupi athu ochimwawa. Ambirife tame-nya nkhondoyi kwa zaka zambiri ndipo Yehova wa-khala akutithandiza. Komabe nthawi zina tingaonekuti tatopa kumenyana ndi adani athu ndiponso ku-yembekezera mapeto a dziko loipali. Komatu tiyene-ra kupitirizabe chifukwa nkhondoyi idakalipo. Yesuananeneratu kuti m’masiku otsiriza ano tidzakuma-na ndi mayesero ndi mavuto ambiri. Koma ana-

APRIL 2016 GAWO 1 19

nenanso kuti tikhoza kupambana ngati titapirira.(Werengani Luka 21:19.) Kodi kupirira n’kutani?Nanga n’chiyani chingatithandize kupirira tikaku-mana ndi mavuto? Kodi tingaphunzire chiyani kwaanthu akale amene anapirira? Nanga kodi tingalo-le bwanji kuti “kupirira kumalize kugwira ntchitoyake”?—Yak. 1:4.

KODI KUPIRIRA N’KUTANI?3 M’Baibulo, mawu akuti kupirira amatanthauza

zambiri. Mawuwa amatanthauza zimene timaganizakomanso zimene timachita tikakumana ndi mavuto.Munthu wopirira amakhala wolimba mtima, wokhu-lupirika komanso woleza mtima. Buku lina linati ku-pirira “n’kukhala ndi mtima wosagonja ukakumanandi mavuto chifukwa chakuti uli ndi chikhulupirirocholimba. Khalidweli limathandiza munthu kukha-labe wolimba pamene akukumana ndi mavuto. Mu-nthu wopirira saganizira kwambiri za mavuto amene3. Kodi kupirira n’kutani?

20 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

akukumana nawo koma amaganizira za madalitsoamene angapeze akapirira mavutowo.”

4 Akhristufe timapirira chifukwa cha chikondi.(Werengani 1 Akorinto 13:4, 7.) Popeza timakondaYehova, timapirira mavuto onse amene timakuma-na nawo pochita chifuniro chake. (Luka 22:41, 42)Abale ndi alongo athu akatilakwira chifukwa chotisi angwiro, timapirira chifukwa choti timawakonda.(1 Pet. 4:8) Komanso kukonda mwamuna kapenamkazi wathu kumatithandiza kuti tizipirira ‘masau-tso’ alionse amene tingakumane nawo m’banja. Ku-matithandizanso kuti tiziyesetsa kulimbitsa banja la-thu.—1 Akor. 7:28.

KODI N’CHIYANICHINGAKUTHANDIZENI KUPIRIRA?

5 Muzipempha Yehova kuti akupatseni mpha-mvu. Malemba amati Yehova ‘amatipatsa mphamvu4. N’chifukwa chiyani tingati chikondi ndi chimene chimatha-ndiza Akhristu kuti azipirira?5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi amene anga-tithandize kwambiri kupirira?

APRIL 2016 GAWO 1 21

kuti tithe kupirira ndiponso amatitonthoza.’ (Aroma15:5) Iye amadziwa chibadwa chathu komanso zi-mene tikukumana nazo ndipo amamvetsa mmenetikumvera. Amadziwanso bwino zinthu zimene zi-ngatithandize. Paja Baibulo limanena kuti: “Anthuamene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo,adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipoadzawapulumutsa.” (Sal. 145:19) Koma kodi Mulu-ngu amayankha bwanji tikamupempha kuti atipatsemphamvu?

6 Werengani 1 Akorinto 10:13. Tikapempha Ye-hova kuti atithandize kupirira mayesero, iye ‘amape-reka njira yopulumukira.’ Kodi ndiye kuti Yehovaamachotsa mayesero athuwo? Nthawi zina amacho-tsadi. Koma nthawi zambiri amangotithandiza kuti‘tithe kuwapirira.’ Yehova amatipatsa mphamvu kuti‘tithe kupirira zinthu zonse, tikhale oleza mtimandiponso tikhale achimwemwe.’ (Akol. 1:11) Po-peza amadziwa zinthu zimene sitingakwanitse,6. Kodi Yehova amapereka bwanji “njira yopulumukira?”

22 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

sangalole kuti vuto likule kwambiri mpaka kufikapoti sitingathe kukhalabe okhulupirika.

7 Muziphunzira Mawu a Mulungu kuti mulimbi-tse chikhulupiriro chanu. Munthu amene akufunakukwera phiri la Everest, lomwe ndi lalitali kwambi-ri padziko lonse, amafunika mphamvu zambiri. Cho-ncho kuti akweredi amafunika kudya chakudya cha-mbiri chopatsa mphamvu. Kuti ifenso tithe kupiriramayesero amene timakumana nawo tiyenera kuphu-nzira kwambiri Mawu a Mulungu. Timafunika ku-dziletsa zinthu zina n’cholinga choti tipeze nthawiyowerenga, kuphunzira komanso kusonkhana. Tika-machita zimenezi timapeza “chakudya chokhalitsa,chopereka moyo wosatha.”—Yoh. 6:27.

8 Muzikumbukira kuti kukhala okhulupirika7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuphunzira kwambiriMawu a Mulungu kumathandiza kuti tipirire?8, 9. (a) Malinga ndi lemba la Yobu 2:4 ndi 5, kodi tiyenerakukumbukira chiyani tikakumana ndi mayesero? (b) Mukaku-mana ndi mayesero, kodi muyenera kuyerekezera kuti mukuo-na ndani?

APRIL 2016 GAWO 1 23

n’kofunika kwambiri. Tikakumana ndi mayesero ti-yenera kukumbukira kuti zimene tingachite zingaso-nyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova kapenaayi. Zimene tingachitezo zimasonyezanso ngati tima-onadi kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Kumbu-kirani kuti Satana ananyoza Yehova ponena kuti:“Munthu angalolere kupereka chilichonse chimeneali nacho kuti apulumutse moyo wake.” Paja pone-na za Yobu iye anauza Yehova kuti: “Tatambasu-lani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpa-ka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’masomuli gwa!” (Yobu 2:4, 5) Ponena zimenezi, Sata-na ankatanthauza kuti palibe munthu amene ama-tumikira Yehova chifukwa chomukonda. Maganizoamenewa adakali nawobe mpaka pano. Tikutero chi-fukwa chakuti patapita zaka zambiri, iye anatha-mangitsidwa kumwamba ndipo pa nthawiyo n’kutiakupitirizabe kuneneza atumiki a Mulungu okhulu-pirika “usana ndi usiku.” (Chiv. 12:10) Choncho

24 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

Satana amaonabe kuti anthufe sitingakhale okhulu-pirika kwa Mulungu ngati titakumana ndi mavuto.Amafunitsitsa kutiona titasiya kumvera Yehova ndi-ponso kumutumikira.

9 Choncho mukakumana ndi mavuto muziyereke-zera kuti mukuona magulu awiri. Mbali ina kuliSatana ndi ziwanda zake ndipo akunena kuti ma-vutowo akakupanikizani musiya kutumikira Yeho-va. Mbali ina kuli Yehova, Yesu, angelo ndiponsoodzozedwa amene anaukitsidwa ndipo onse akuku-chemererani. Iwo akusangalala chifukwa choti tsikulililonse mukuyesetsa kupirira ndipo mukusonyezakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Ndiyenomukumva Yehovayo akukuuzani kuti: “Mwana wa-nga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wa-nga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy.27:11.

10 Muziganizira madalitso amene mudzalandiremukapirira. Tiyerekezere kuti mukuoloka mtsinje10. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikakumana ndi mavuto?

APRIL 2016 GAWO 1 25

waukulu ndipo mwafika pakati pa mtsinjewo. Muka-yang’ana kutsogolo mukuona kuti padakali mtundawautali kuti mukafike kutsidya. Koma simukubwere-ra m’mbuyo chifukwa muli ndi chikhulupiriro kutimukapitiriza kuoloka, mufika kumtunda. Mavutoamene timakumana nawo angafanane ndi zimene-zi. Yesu atakumana ndi mavuto anamvanso chimo-dzimodzi. Iye ananyozedwa komanso anamva ulu-lu kwambiri atakhomeredwa pamtengo. Koma kodin’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Baibulo li-mati iye ankaona “chimwemwe chimene anamuikirapatsogolo pake.” (Aheb. 12:2, 3) Ankaganizira ma-dalitso amene adzapeze akapirira. Ankaona kuti ku-pirira kwake kuthandiza kuti dzina la Yehova liye-retsedwe komanso kutsimikizira kuti Yehova ndiyewoyenera kulamulira. Ankadziwanso kuti mavutowondi akanthawi koma madalitso amene adzapeze ndiamuyaya. Masiku ano nafenso tingakumane ndi ma-vuto aakulu koma tizikumbukira kuti mavutowa ndiakanthawi.

26 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

“AMENE ANAPIRIRA”11 Tiyenera kukumbukira kuti si ife tokha ame-

ne tikukumana ndi mayesero. Paja Petulo analimbi-kitsa Akhristu amene ankakumana ndi mayeserokuti apirire. Iye anawauza kuti: “Khalani olimbam’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye, podziwakuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dziko-li akukumana ndi masautso ngati omwewo.” (1 Pet.5:9) Zitsanzo za “amene anapirira” zimatithandi-za kudziwa zimene tingachite kuti nafenso tipirire.Zimatitsimikiziranso kuti nafenso tingathe kupiri-ra ndipo tidzadalitsidwa tikakhalabe okhulupirika.(Yak. 5:11) Tiyeni tsopano tikambirane zitsanzo zi-ngapo.[1]

12 Akerubi. Adamu ndi Hava atachimwa, Yehova‘anaika akerubi kum’mawa kwa munda wa Edeni.Anaikanso lupanga loyaka moto limene linali kuzu-11. Kodi kuganizira zitsanzo za “anthu amene anapirira” ku-ngatithandize bwanji?12. Kodi tikuphunzira chiyani kwa akerubi amene ankalonde-ra munda wa Edeni?

APRIL 2016 GAWO 1 27

ngulira mosalekeza potchinga njira yopita kumtengowa moyo.’[2] (Gen. 3:24) Zimene akerubiwa anachi-ta zingatithandize kuti nafenso tizipirira tikapatsi-dwa ntchito yovuta potumikira Mulungu. Mulungusanalenge akerubi kuti azigwira ntchito yolonderayindipo sichinali cholinga chake kuti anthu adzachi-mwe. Koma Adamu ndi Hava atachimwa akerubiwaanagwira ntchitoyi mosanyinyirika. Anachita zime-nezi ngakhale kuti anali ndi udindo waukulu kwa-mbiri kumwamba. Iwo anagwira ntchitoyi mokhulu-pirika mpaka mapeto. N’kutheka kuti anaigwira kwazaka zoposa 1,600 ndipo inatha pa nthawi ya Chigu-mula.

13 Yobu. Zimakhala zowawa kwambiri ngatimnzathu kapena wachibale watilankhula mawuopweteka, ngati tikudwala matenda aakulu kape-na ngati munthu amene timamukonda wamwalira.Koma chitsanzo cha Yobu chikhoza kutilimbikitsa13. Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu kuti apirire mayeseroamene anakumana nawo?

28 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

zoterezi zikachitika. (Yobu 1:18, 19; 2:7, 9; 19:1-3)Yobu sankadziwa chimene chinayambitsa mavutoake koma anakhalabe wokhulupirika. Kodi n’chiya-ni chinamuthandiza kuti apirire? N’chifukwa cha-kuti ‘ankaopa Mulungu.’ (Yobu 1:1) Yobu ankafu-nitsitsa kusangalatsa Yehova zivute zitani. Yehovaanamuthandiza ndipo iye ankaganizira zinthu zo-chititsa chidwi zimene Yehova anachita pogwiritsantchito mzimu woyera. Yobu ankadziwa kuti Yeho-va adzathetsa mavuto akewo pa nthawi yoyenera.(Yobu 42:1, 2) Ndipo izi n’zimene zinachitikadi. Ba-ibulo limanena kuti: ‘Yehova anathetsa masautso aYobu ndipo anayamba kum’patsa zonse zimene ana-li nazo, kuwirikiza kawiri.’ Limanenanso kuti Yobu“anamwalira ali wokalamba ndiponso wokhutira ndimasiku ake.”—Yobu 42:10, 17.

14 Mtumwi Paulo. Kodi mukuzunzidwa chifu-kwa chotumikira Mulungu? Kodi ndinu mkulu ka-14. Kodi lemba la 2 Akorinto 1:6 likusonyeza kuti kupirirakwa Paulo kunathandiza bwanji Akhristu anzake?

APRIL 2016 GAWO 1 29

pena woyang’anira dera ndipo mukuona kuti mulindi ntchito yambiri? Chitsanzo cha Paulo chinga-kuthandizeni. Iye anakumana ndi mavuto aakuluochokera kwa adani ake komanso ankadera nkhawakwambiri za abale ndi alongo a m’mipingo yonse.(2 Akor. 11:23-29) Koma Paulo sanafooke ndipochitsanzo chake chinalimbikitsanso ena. (Werenga-ni 2 Akorinto 1:6.) Ngati inunso mukukumana ndimavuto enaake, dziwani kuti mukakhalabe okhulu-pirika mukhoza kulimbikitsa Akhristu anzanu.

KODI MUMALOLA KUTI “KUPIRIRAKUMALIZE KUGWIRA NTCHITO YAKE”?15 Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupiri-

ra kumalize kugwira ntchito yake.” Kodi kupirirakumamaliza kugwira “ntchito” iti? Kumatithandizakukhala “okwanira ndi opanda chilema m’mbali zo-nse, osaperewera kalikonse.” (Yak. 1:4) Mayesero15, 16. (a) Kodi kupirira kumamaliza kugwira “ntchito” yo-tani? (b) Kodi tingatani “kuti kupirira kumalize kugwira ntchi-to yake”? Perekani zitsanzo.

30 GAWO 1 NSANJA YA OLONDA

amatithandiza kudziwa mbali zimene sitichita bwi-no. Koma tikapirira mayeserowo tingati timakhalaokwanira mbali zonse. Mwachitsanzo, tikakumanandi mayesero n’kupirira, timaphunzira kukhalaoleza mtima, oyamikira komanso achifundo.

16 Kupirira kumatithandiza kuti tikhale Akhristuokhulupirika. Choncho tikakumana ndi mayesero ti-samagonje n’kusiya kutsatira mfundo za m’Baibulon’cholinga choti mavuto athuwo athe. Mwachitsa-nzo, kodi mungatani ngati mukuyesetsa kuti mu-samaganizire zinthu zoipa? Simuyenera kugonja.M’malomwake muyenera kupemphera kwa Yehovakuti akuthandizeni kuthana ndi vutolo. Zikatere mu-maphunzira kukhala odziletsa kwambiri. Nanga mu-ngatani ngati mukutsutsidwa ndi wachibale wanuamene si wa Mboni? Musagonje ndipo pitirizani ku-tumikira Yehova ndi mtima wonse. Zimenezi zinga-chititse kuti muzidalira kwambiri Yehova. Musaiwa-le kuti tikamapirira mayesero, Yehova amatidalitsa.—Aroma 5:3-5; Yak. 1:12.

APRIL 2016 GAWO 1 31

17 Tiyenera kupirira osati kwa kanthawi chabe,koma mpaka mapeto. Tiyerekeze kuti anthu akwerasitima ndipo ikumira. Kuti munthu apulumuke, aye-nera kusambira mpaka kumtunda. Ngati munthuwasambira kwa nthawi yaitali koma n’kutopa atatsa-la pang’ono kufika pamtunda akhoza kufa mofananandi munthu amene anangosambira pang’ono n’kusi-ya. Mofanana ndi zimenezi, kuti tidzalowe m’dzi-ko latsopano tiyenera kupirira mpaka mapeto. Tiye-nera kukhala ndi maganizo amene mtumwi Pauloanali nawo. Kawiri konse iye anati: “Sitikubwereram’mbuyo.”—2 Akor. 4:1, 16.

18 Tisamakayikire kuti Yehova atithandiza kupiri-ra mpaka mapeto. Paja Paulo ananena kuti: “Ti-kugonjetsa zinthu zonsezi kudzera mwa iye ameneanatikonda. Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa,moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu17, 18. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tiyenera ku-pirira mpaka mapeto. (b) Kodi tisamakayikire za chiyani ma-siku otsiriza ano?

wlp

16

.04

-CN

-11

51

22

2

32 NSANJA YA OLONDA

Pangani sikani kachidindo aka kapenapitani pa webusaiti yathu ya

www.jw.org/ny5

zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu, msinkhu,kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, si-chidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulunguchimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”(Aroma 8:37-39) N’zoona kuti nthawi zina timato-pa, koma tiyeni tipitirize kupirira mpaka mapeto. Ti-katero nafenso tidzakhala ngati Gidiyoni ndi asilikaliake amene anapitirizabe ‘kuthamangitsa adani awo.’—Ower. 8:4.

�����������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������

MAWU AKUMAPETO:[1] (ndime 11) Kuganizira zitsanzo za anthu amene apiriramasiku ano kukhoza kukuthandizaninso. Mwachitsanzo mu-ngawerenge Buku Lapachaka lachingelezi la 1992, 1999, ndila 2008 komanso kabuku kakuti, Mboni za Yehova M’Ma-lawi kuti mumve za abale athu amene anapirira ku Ethiopia,ku Malawi ndi ku Russia.[2] (ndime 12) Baibulo silitchula kuti akerubi amene anka-londera mundawu analipo angati.